Bungwe la Super League of Malawi (SULOM) lasuntha masewero awiri amu TNM Supa ligi sabata ino kufikira mmasiku osadziwika pomwe matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers atumiza osewera ochuluka ku timu ya Flames.
Bungweli lachita izi litakana koyamba kuti masewero onse amu ligi achitika mu sabata ino koma tsopano bungweli lati masewero a Mighty Mukuru Wanderers ndi MAFCO komanso Silver Strikers ndi Extreme FC sachitika kamba koti Silver ndi Noma anatumiza osewera anayi ku Flames.
Koma ngakhale FCB Nyasa Big Bullets inatumizanso nambala ya osewera omwewa, timuyi yati isewerabe masewero awo ndi Blue Eagles lamulungu likudzali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores