BLUE EAGLES YATCHAYIDWA MMIMBA
Timu ya Blue Eagles yayenera kukhala modandaula pomwe osewera awo atatu, Micium Mhone komanso magoloboyi awiri odalilika, Brighton Munthali ndi John Soko sapezeka kutimuyi mpaka kumapeto kwa ligi ya chaka chino.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi ndipo yati Munthali akulowera ku South Africa kutimu ya Black Leopards pa ngongole ya chaka chimodzi pomwe Mhone ndi Soko apita kumaphunziro a miyezi isanu ndi umodzi (6) ku sukulu ya apolisi ku Blantyre.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Christopher Sibale anati ziwakhudza kwambiri koma atenga goloboyi mmodzi kutimu yawo yachisodzera kuti akakhale limodzi ndi Chakonda Majanga yemwe anali wachitatu kutimuyi.
Ena mwa omwe atenge nawo mbali pa maphunzirowo ndi osewera akale, Stuart Mbunge, Charles Ngosi, Chimwemwe Kalanje, Steven Chagoma, Wongani Ngulube, Maxwell Salambula, Japhet Mambelera, Aubrey Mayuni ndi Dan Phiri.
All the best
Thanks for the information
Thanks for your information
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores