"BANGWE INATULUKA KALE MU LIGI" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wati ndi odandaula poti timu yake yagonja ndi Bangwe All Stars yomwe akuti inatuluka kale mu ligi ngakhale yachoka ku chigwa cha matimu otuluka loweruka.
Timuyi inagoletsetsa chigoli chapa mphindi ziwiri cha Madalitso Chiume chomwe chinali chokwana kupambanitsa Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira 1-0.
Atatha masewero, mphunzitsi wa Moyale anali okwiya ndi kayimbilidwe ndipo anati Bangwe inatuluka Kale.
"Tinasewera bwino koma ndizodandaulitsa kuti taluza ndi timu yotuluka kale, Bangwe ndinayitulutsa kale mu ligi. Red card ija simayenera chifukwa choti MacDonald Harawa ndi captain, ndi amene amayenera kumuyankhula ref koma anthu amangoti kumpoto koma izi ndaona ku Blantyre ndadziwa kuti oyimbira onse amasewera nawo." Anatero Mhango.
Kutsatira kugonjaku, Moyale ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi 16 pa masewero 12.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores