KHUDA WASIYANA NDI POLOKWANE
Bwalo lalikulu ku South Africa la Gauteng High Court lagamula kuti katswiri wa Flames, Khuda Muyaba ndi timu ya Polokwane City alekana kutsatira kuthetsa kwa mgwirizano wawo.
Muyaba watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati iye ndiyemwe anakapereka pempho ku bwaloli kamba kosemphana ndi timuyi.
"Nditha kutsimikiza ndithu kuti zatheka. Apapa ndine free agent.” iye anauza tsamba la Wa Ganyu.
Khuda wati sakubwereranso ku Malawi ndipo matimu angapo aku South Africa akumufuna katswiriyu. Ena mwa iwo ndi Royal AM ndi Black Leopards omwe amveka kuti akumufuna katswiriyu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores