"CHIZUNGU CHIKUFUNIKIRA PA ANTHU" - LIWEWE
Mmodzi mwa atolankhani a nkhani zamasewero mdziko muno, Steve Liwewe Banda, wati makono anthu akufunikira kudziwako kachingerezi pang'ono ndi cholinga choti azilumikizana ndi anthu ammayiko osiyanasiyana poti chiyankhulochi chimagwiritsidwa ntchito mmayiko ambiri.
Liwewe amayankhula izi kutsatira katswiri wa timu ya Flames, Alick Lungu, anakanika kuyankhula mu chingerezi pomwe anasewera bwino mmasewero atimuyi ndi Zambia ku COSAFA ndipo James Sangala ndiye amamutanthauzira.
Liwewe wati ndi zofunika kuti anthu adziweko ngakhale pang'ono chingerezi poti zinthu zambiri monga kufunsira ntchito, kukambirana mu nyumba ya malamulo komanso ndondomeko za mankhwala ndi zina zimakhala mchingerezi.
"Kumangofunika kudziwako chingerezi pang'ono ngakhale utaphotchola amvabe kuti ukufuna chiyani. Chosangalatsa pano nchakuti ife makolo ngakhale sukulu inativuta timayesetsa kuti ana athu aphunzire chizungu." Anatero Liwewe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores