Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
SINGINI WAPATSIDWA K100,000 POSEWERA BWINO NDI BULLETS
Mmodzi mwa masapota a timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Mphatso 'Monty' Howahowa apereka ndalama zokwana K100,000 kwa katswiri wapakati watimuyi, Blessings Singini kamba kosewera bwino pomwe timuyi imasewera ndi FCB Nyasa Big Bullets loweruka lapitali.
Howahowa anapereka ndalamayi lachiwiri pomwe anapita komwe timuyi imachita zokonzekera pa masewero awo ndi Karonga United kumathero a sabatayi.
Poyankhulapo atapereka ndalamayi, Howahowa anati wapereka ndalamayi kuti osewerayu apitilize kulimbikira komanso kumenyera nkhondo timuyi kuti izichita bwino.
"Osewera angapo anasewera bwino kwambiri ndipo Singini anali mugulu lomwelo ndipo inali Derby yake yoyamba koma anasewera mwapamwamba nde ndinasankha kumupatsa ndalamayi pomuthokoza ndi mmene anachitira koma kumulimbikitsa pamodzi ndi osewera enanso kutimuyi." Anatero Howahowa.
Awa anali masewero achitatu a Singini kusewera kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers ndipo achiwiri kumaliza o
SINGINI NDI THANTHWE LA EKWENDENI
Katswiri wa Ekwendeni Hammers, Blessings Singini, akuchita bwino kwambiri pomwe wagoletsa zigoli zinayi mmasewero atatu otsogozana omwe Ekwendeni Hammers yasewera.
Singini amasewera pakati motchinga kutimuyi ndipo ntchito yogoletsa singakhale kwambiri ya iyeyu koma anagoletsa chigoli chomwe chinapambanitsa Hammers pomwe imamenya ndi Extreme FC sabata yatha.
Iye anagoletsa zigoli ziwiri pomwe ankamenya ndi Airborne Rangers mmasewero amu FDH Bank Cup ndipo sabata ino, chigoli chake chatengera timuyi pa nambala yachinayi pomwe waipambanitsa 1-0 ndi Blue Eagles.
Iye walowa mmalo mwa Mphatso Magaleta yemwe amagoletsera kwambiri timuyi koma pano iye ndiye mutu wa timuyi.