BULLETS ISEWERA CAF CHAMPIONS
Akatswiri achikho cha TNM Supa ligi, FCB Nyasa Big Bullets asewera nawo mu mpikisano wa CAF Champions league wachaka chino pomwe bungwe la Confederations of African Football lavomereza pempho lawo lotenga nawo mbali mu mpikisanowu.
Mkulu oyang'ana za club licensing ku bungwe la Football Association of Malawi, Cassper Jangale, wati Bullets inakonza zonse zoyenereza zofunika kutenga nawo mbali mu mpikisanowu ndipo wayamikira timuyi poti mpikisanowu ukuthandiza osewera kuzigulitsa mmatimu akunja.
Timuyi ili ndi mwayi wowonjezera osewera pomwe CAF ikhale ikulandira mayina omwe matimu agwiritse ntchito kuchokera pa 1 July mpaka pa 31 August ndipo mmodzi mwa akuluakulu a timuyi, Albert Chigoga wati adikira mawu a aphunzitsi kutimuyi.
"Munthu ukamapita ku nkhondo, umafunikira kutenga zida zamphamvu nde ngati aphunzitsi afune kuonjezera, ife titsatira kutero."
Bungwe la CAF yati matimu opambana ndime yachipulula yayamba azifika mmagulu kulekana ndi poyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores