EAGLES ILANGA OSEWERA OTHAMANGITSA OYIMBIRA
Timu ya Blue Eagles yati ipereka chilango kwa osewera aliyense amene anakhuzidwa ndi mpungwepungwe umene unachitika pakutha pa masewero a timuyi ndi Ekwendeni Hammers mu ligi ya TNM ku Mzuzu la mulungu lapitali.
Mlembi wamkulu wa timuyi, Benjamin Msowoya, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mchitidwewu wayipitsa mbiri ya nthambi yopereka chitetezo ya Police.
Iye wati akuluakulu a nthambi ya Polisi mdziko muno yati osewera omwe anathamangitsa oyimbirawa alandire chilango kamba kosowa khalidwe.
Eagles inagonja masewerowo ndi Ekwendeni Hammers 1-0 ndipo osewera anathamangitsa oyimbira mpira Rose Zimba ndi omuthandizira ake mcholinga choti awamenye ati posakhutira nawo kuti sanagwire ntchito yawo bwino. Izinso zinachititsa kuti apolisi aponye utsi wokhetsa Misonzi pa bwalo la Mzuzu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores