Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Gracinda wawina K10,000πΈ atalosera molondolaπ― magemu 5 pa Owinnaβ½ sabata yatha Monday 19 - Sunday 25 Jun. π
Nanu loserani magemu ambiri pa Owinna.com kuti muchulutse mwayi wowina ma 10 pin sabata iliyonse.
MON MANOMA ANZANGA Ndangonva kt alex ngwira / balikinyo mwakanyongo kmanso francirco mandinga ndiye ndanva kt gerard phiri njunio akubwelakonso amene mukuziwainu tanenani
Kodi mado game yazuro ndizoona ndimmene tikamenyela munja zoona ndikoyenera kuthanawo dro nanga menetikamenyera muja akana khara iwowo akanatinya zingati nanga ikangakhara sirinva ikanatitinya zingati
log table yanu ndi yolakwika ntaja rangers ilu pa number 6 osati 5
Fixtures
yasani moto maule kuthamangila thawi
wiki ino maule amenya ndi iti?
Admin onani pama game azulo i predicted that will end 2-1 in favour of red lions
Video mbc
MPINGANJIRA WAOPSEZA KUCHOTSA THANDIZO KU WANDERERS
Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, awopseza kuti asiya kuthandiza timuyi pompopompo ngati ochemerera atimuyi angapitilize mchitidwe opangira nkhanza osewera atimuyi ngati sanachite bwino.
Mpinganjira wayankhula izi kutsatira kuyendetsa pansi kwa osewera atimuyi ndipo ena analawako makofi pomwe anafanana mphamvu ndi Dedza Dynamos 1-1 sabata yatha.
Iye wati umoyo wa osewera ndi ofunika ndipo akuyenera kutetezedwa.
"Sizinali zabwino poti osewera aja anali pa chiopsezo, zikadzangochitikanso zoletsa osewera kukwera bus yawo, ndidzaleka pompopompo kuthandiza timuyi." Anatero Mpinganjira.
Mkuluyu wakhala akuthandiza timuyi kwa zaka zingapo tsopano ndipo pakadali pano amapereka K410 million pa chaka kudzera mwa kampani ya Ekhaya Foods.
Katswiri wakale wa FCB Nyasa Big Bullets, Chimwemwe Idana, akhalabe kutimu ya Silver Strikers kutsatira kulengeza kwa timuyi kuti katswiriyu amaliza ligi ya chaka chino.
Timu ya Silver Strikers yalengeza usiku wa lachisanu mothokoza akuluakulu a timuyi pokambirana ndi timu ya Mbeya City zotenga katswiriyu.
Idana wakhala wofunikira kutimuyi pomwe wagoletsa zigoli zinayi ndikuthandizira zina zisanu ndi chimodzi (6).
PHIRI JR LEAVES AL HILAL
Flames midfielder, Gerald Phiri Jr, has parted ways with Sudanese side, Al Hilal Omdurman following the end of his contract at the team.
He joined the team in 2021 after his Contract expired with Baroka FC of South Africa and through his Facebook page, has wished the team all the best for the future.
His playing time at the club became limited in his final year due to injuries but enjoyed his first year at the team. So far, he has not communicated about his next move despite Mighty Mukuru Wanderers supporters begging his to return to his boyhood club.
"DE JONGH AKAPHUNZIRE MPIRA WAKU MALAWI" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald 'Nginde' Mtetemera, wati akupita ku Lilongwe ndi cholinga chimodzi chokatenga ma points atatu basi pomwe akukumana ndi Silver Strikers mu ligi ya TNM loweruka pa bwalo la Bingu.
Mtetemera wati alibe mantha aliwonse kukumana ndi ma Banker ndipo akonzekere kusenza thumba la misomali pomwe iye akamuphunzitse waku mpanje.
"Timu ilibwino ndipo chilichonse chili mchimake, ulendo tanyamuka kuti tikapeze chipambano tizibwerako. Uyu [De Jongh] samaudziwa mpira waku Malawi ndipo loweruka lino akawudziwa mmene umaseweredwera." Anatero Nginde.
Timu ya Chitipa United inapereka mabala owawa kumatimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets pomwe anawathira kugonja kwawo koyamba chaka chino mu ligi. Timu ya Silver ndi yokhayo imene sinalaweko kugonja ndipo ikupita masewerowa ikutsogola ndi 24 points pa nambala yoyamba kusiyana ma points asanu ndi atatu (8) ndi Chitipa United.
MUYABA TRAINING WITH MADUKA'S ROYAL AM
Reports from South Africa have indicated that Flames controversial player, Khuda Muyaba, has been training with John Maduka's Royal AM ahead of the 2023/24 DSTV Premiership season.
This comes after his relationship with his side, Polokwane City, turned sour and was not part of the team that helped it's promotion back into the top as he left the club early this year.
Meanwhile, the reports are in agreement with what the star wrote on Thursday that he can not play for local clubs as people think in Malawi now.
He will be the first Malawian signing for Malawian Coach, John Maduka if it happens to impress him during this time. Muyaba won the golden boot in Malawi in 2019 after netting 21 goals and missed it by just a goal in 2021 in the Glad African Championship with Polokwane City.
THOM WAPITA KU TP MAZEMBE
Katswiri wa Scorchers, Sabina Thom, atumikira timu ya amayi osewera mpira wamiyendo ya TP Mazembe yaku DRC pomwe wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi.
Katswiriyu anachoka sabata yatha kupita kutimuyi komwe amakayesetsa zachipatala ndipo wakhonza komanso timu yake ya MDF Lionesses yatsimikiza za nkhaniyi. Poyankhula ndi Thom, iye wati ndi okondwa kupita ku timuyi.
"Ndi zokoma kwambiri ndipo ndine osangalala kukhala mbali imodzi ya timu ngati iyiyi ndipo anali maloto anga kutumikira timu yaikulu ngati TP Mazembe." Anafotokozapo Thom.
Katswiriyu wakhala ofunikira kumbali ya Scorchers pomwe anaithandiza kufika mu ndime yotsiriza mu mpikisano wa COSAFA Women's Championship. Iye amasewera pakati chakumanja kapenanso kutsogolo ndipo ndi msilikali wa dziko lino.
Akuluakulu a timu ya Mighty Mukuru Wanderers ayimitsa katswiri wawo wapakati, Alfred Manyozo Jr, kufikira bata libwere kutimuyi.
Timuyi yachita izi pofuna kuteteza umoyo wa osewerayu kamba koti ochemerera atimuyi anafuna kumumenya osewerayu ati pomuganizira kuti zolakwika zonse zakutimuyi anayambitsa ndi iyeyo.
Timuyi ibwera ndi dongosolo lonse kutsogoloku.
Hahahah koma ndaseka π€£π€£π€£ππππππ
HADJI WALI WASOWANSO KU BANGWE
Malipoti amveka kuti katswiri wakale wa Silver Strikers ndi FCB Nyasa Big Bullets, Hadji Wali sakupezeka kuzochitika za timuyi kwa masabata atatu tsopano.
Izi zadziwika pomwe limodzi mwa tsamba lolemba nkhani zamasewero mdziko muno la Wa ganyu lalemba za nkhaniyi ndipo anayankhulana ndi team manager watimu, Steve Madeira.
"Chomwe ndikudziwa ndi choti osewerayu akumapezeka koma mphunzitsi watimuyi ndi yemwe akumamubwenza kuti azipita. Sindikudziwa kuti ndi chani koma akumabwenzedwa." Anatero Madeira.
Katswiriyu wakhala akuchotsedwa ku Silver komanso ku Bullets kamba kosowa khalidwe.
Too bad
"OSOKONEZA PA MASEWERO A BULLETS NDI WANDERERS ANJATIDWA" - MWAMADI
Mtsogoleri wa masapota a FCB Nyasa Big Bullets, Stone Mwamadi, walangiza masapota amatimu m'dziko muno kuti azivomereza matimu awo akagonja osati kuchita ziwawa.
Malingana ndi a Mwamadi , ati otsatira matimu m'dziko muno akuyenera kudziwa kuti mumpira mumakhala kugonja, Kupambana komanso kulepherana .
Iwo amayakhula izi kutsatira zomwe otsatira timu ya Mighty Mukuru Wanderers akhala akuchita kwa osewera awo masabata awiri apitawo kaamba koti timuyi sikuchita bwino.
Otsatira timu ya Mighty Mukuru Wanderers sabata yatha analetsa osewera a timuyi kukwera Bus yatimuyi atalepherana 1-1 nditimu ya Dedza Dynamos Salima Sugar FC pabwalo la kamuzu stadium.
A Mwamadi, achenjeza otsatira matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Nyasa Big Bullets kuti yemwe angakapezeke akuchita zosokoneza masewero a Blantyre Derby omwe alipo loweruka lino adzanjatidwa, ndipo adzalandira chilango.
Katswiri wa kale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers ndi Flames, Joseph Kamwendo tsopano watenga tsamba la uphunzitsi wa mpira wamiyendo la CAF C kutsatira kukhoza mayeso a pepalali.
Team manager watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Robert Ng'ambi tsopano ali ndi pepala la maphunziro a uphunzitsi wa mpira wamiyendo la CAF C kutsatira kukhoza mayeso a tsamba la Diplomali.
CONFIRMED: BULLETS VS YANGA ON 6 JULY
TNM Super League Champions, FCB Nyasa Big Bullets will play Tanzanian Champions, Young Africans at the independence day celebration on 6th July as per reports found by Owinna.
This comes after a change of consideration after northern region side, Chitipa United was set to entertain people on the day by playing Mighty Mukuru Wanderers.
After too many rumours and tips, it is confirmed that the People's team will play YANGA FC in front of President, Lazarus Chakwera. This is the third time this season the team is asked to participate in special games after playing Silver Strikers twice on Kamuzu Day and Castel Cup launch.
"MASAPOTA A KU CHITIPA NDI OZINDIKIRA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald'Nginde'Mtetemera wati masapota atimu yake ndi ozindikira kusiyana ndi masapota a matimu ena pomwe wati amamvetsetsa zotsatira za masewero.
Mtetemera amayankhula izi atatha masewero awo pomwe anagonja 1-0 ndi Dedza Dynamos pa bwalo la Karonga kuti atuluke mu chikho cha FDH Bank lachitatu. Iye anati ochemerera atimuyi samawafinya kwambiri kuti azichita bwino poti timu yawo ikadali ya ana.
"Kwa masapota aku Chitipa ndi ozindikira kusiyana ndi amatimu enawa ndipo amadziwa kuti kumpira kuli kupambana, kufanana mphamvu ndi kugonja nde lero tagonja, tachivomereza. Ndimanena mobwereza kuti timu yathu ndi yachisodzera nde tikadaphunzirabe, mwina zimangochitika tikapambana kuti mwina tsiku limenelo kwacha bwino nde sindimayembekezera zambiri kwa anyamatawa." Anatero Nginde.
Mtetemera anayankhula izi pomwe masapota a Mighty Mukuru Wanderers akumachitira za ntopola osewera awo akagonja kapena kufa
Afcon fixture
Fixture today
"MANYOZO IS ONE OF THE BEST DEFENDING MIDFIELDERS" - KAYIRA
Bangwe All Stars midfielder, Chimango Kayira has saluted Mighty Mukuru Wanderers' midfielder, Alfred Manyozo Jr, saying he has been one of his toughest competitors in the League.
Kayira wrote this on his Facebook page amidst attacks from the Nomads supporters on Manyozo saying he should disappear from any operations of the team and that he is the main causer of the team's misfortunes. The star was partly beaten as the team drew 1-1 with Dedza Dynamos last week and Kayira says Manyozo has worked with passion at the team.
"Alfred Manyozo has always been one of my toughest competitors throughout the years. I remember our derby days when I was at Bullets, we used to take moments to plan on how to block his long vision. His passing range has always been inch perfect. One of the best defending midfielders of our generation."
"His track record is remarkable. 15 years of service to the Blue camp. A man of decency and compassion.
OSEWERA ASANU NDI AWIRI A BULLETS SAPEZEKA NDI WANDERERS
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Callisto Pasuwa wati sakhala ndi anyamata ake asanu ndi awiri (7) pomwe timuyi ikumane ndi Mighty Mukuru Wanderers mu TNM Supa ligi loweruka likudzali.
Pasuwa amayankhula izi ndi olemba nkhani a timuyi patsogolo pa masewerowa ndipo wati Eric Kaonga walowanso mu gulu a osewera ena asanu ndi mmodzi omwe sanapezeke mmasewero a Kamuzu Barracks.
"Eric Kaonga nayenso wavulala ndipo Nickson Nyasulu, Chinedu Okafor ndi Yankho Singo ayamba zokonzekera zofewerako pomwe Mike Mkwate, Clyde Senaji ndi Stanley Biliati akanasowabe kwa masabata angapo kutsogoloku." Anatero Pasuwa.
Timu ya Bullets ili pa nambala yachiwiri mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 21 ndipo ikutsogola ndi mapointsi atatu pamwamba pa Wanderers yomwe ikubwera pachitatu.
GANGATA SHOOTS IN SOLDIERS HANDS
The Chipiku Premier Division league outfit Combat Support Battalion FC on Wednesday 28th June 2023 received a morale booster from Masters group of companies ahead of the kick off of the second round of the preliminary round this coming weekend.
The team has received donation of assorted sports equipment namely; 6 football balls, 16 cons, 1 ladder, 12 boots and 2 sets of bibs just to mention but a few worth MK2.5 million.
Support Battalion FC are on second position with 14 points from 7 games in the 2023 Chipiku Premier division league group B 1 point a draft leaders Leyman Panthers FC. They kick start the second round of the preliminaries against Dwangwa United FC at home on Sunday.
Ili ndi bwalo la Ntcheu lomwe likumangidwa ndipo limayenera kutha chaka Chatha ndipo pakatipa linayima kamba koti ndalama zomwe anayika kuti zigwire ntchitotuikuyenda zinatha.
Bwaloli lizidzatenga anthu okwana 20,000 likadzatha.
Ili ndi bwalo la Thyolo lomwe linaikidwa kuti lidzakhala litatha mu February chaka chino komatu mpaka pano siyinathetu.
KUMWEMBE AND KAMANGA TO JOIN FLAMES CAMP
Mighty Mukuru Wanderers talisman, Christopher Kumwembe and Silver Strikers' captain, Chikondi Kamanga are some of the notable faces that will join the Flames camp on Sunday ahead of the COSAFA Cup.
One of the country's online Sports publisher, Wa ganyu that their sources has provided them with names that will join the camp in preparations for the tournament. Here are players:
Nickson Mwase Christopher Kumwembe Clement Nyondo Stanley Sanudi Chimwemwe Idana Dan Chimbalanga Clever Mkungula Kelvin Banda Gaddie Chirwa Mphatso Kamanga Innocent Nyasulu Blessings Mpokera Lawrence Chaziya Mark Lameki Chikumbutso Salima Robert Saizi Lanjesi Nkhoma Alick Lungu Frank Willard Brighton Munthali Ernest Petro Patrick Mwaungulu Crispin Mapemba Loyd Aron Chikondi Kamanga Patrick Macheso Blessings Singini Wongani Lungu
KODI SULOM NDI MWANO KAPENA ZIWINDI?
Bungwe la Super league of Malawi (SULOM) laumilirabe kuchititsa masewero a pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu angakhale kuti bungwe la Football Association of Malawi linaletsa masewero ngati awa pa bwaloli.
Bungwe la FAM linayankhulapo kuti cholakwika chidzachitike pa masewerowa chisadzawakhudze ndipo SULOM yati sikusinthabe masewero aliwonse ndipo aseweredwa mmene ayikidwira.
Izi zapereka mafunso ochuluka kwa anthu osiyanasiyana pa mmene mabungwe awiriwa amagwilira pomwe ubale sukuoneka pakati iwo.
OSEWERA A EXTREME ANASIYA ZOKONZEKERA ATAGWEBA MANOMA
Mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wadandaula ndi mchitidwe wa osewera ake omwe akumazikweza akachita chinthu chapamwamba pomwe akumasiya kuchita zokonzekera za timuyi.
Kafoteka amayankhula izi lamulungu atagonja 1-0 pakhomo ndi Ekwendeni Hammers mu TNM Supa ligi. Iye wati anaona khalidwe lachilendo atagonjetsa Mighty Mukuru Wanderers mmasabata awiri apitawo.
"Ndi zachilendo ndipo sindinazionepo zikuchita angakhale ine ndikusewera mpira kuti kusiya training kamba koti agonjetsa timu yaikulu." Anatero Kafoteka.
Iye walangiza osewerawa kuti asewerere tsogolo lawo mu mpira osati ndalama chifukwa atha osapita patsogolo. Extreme ili pa nambala 16 pomwe ndi pansi penipeni pa ligiyi ndi mapointsi asanu okha.
CHESTER WAUZA MANOMA KUTI SAKUBWERA POSACHEDWA
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Yamikani Chester, wauza mmodzi mwa ochemerera atimuyi kuti sangabwerere kutimuyi kamba koti ali ku ntchito.
Izi zadza pomwe masapota atimuyi anakhamukira ku tsamba la katswiriyu ati kumupempha kuti abwerere kutimuyi pomwe zotsatira sizikuoneka bwino mu ligi ya chaka chino.
Koma poyankhapo, Chester anauza mmodzi mwa ochemererawa kuti iye sangafike kutimuku pano.
"Ndikanali Kaye ku ntchito bwana." Anatero Chester.
Katswiriyu anachoka kutimuyi kumayambiliro kwa chaka chino pomwe sanamvane ndi timuyi nkhani za mgwirizano wake ndipo iye akutumikira timu ya Costa do Sol yaku Mozambique.
MABEDI WAKONDA SINGINI
Mphunzitsi watimu ya Flames, Patrick Mabedi, akuyang'ana zoitana mtsogoleri wa timu ya Ekwendeni Hammers, Blessings Singini, kuti akatumikire mu timuyi ku COSAFA Cup ku South Africa.
Mabedi akufuna katakweyu yemwe wachita bwino kwambiri chaka chino ndi timuyi posewera pakati mmasewero onse omwe timuyi yasewera.
Singini wakhala katswiri wosewera bwino mmasewero awiri chaka chino ndipo mu sabata yangothayi, wagoletsa zigoli zitatu pa masewero awiri ndi Extreme FC komanso Airborne Rangers
FAM NDI SULOM ALI PA MKULIRANO
Bungwe la Football Association of Malawi (FAM) lati cholakwika chilichonse chomwe chidzachitike pa masewero a FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers zisadzawakhudze pomwe bungwe la Super League of Malawi layika masewero pakati pa matimuwa pa bwalo la Kamuzu lowerukali.
Izi zadza pomwe bungwe la FAM linaletsa masewero akuluakulu pa bwaloli poti silili bwino koma SULOM yachita mosemphana ndi zimenezi. Mlembi wamkulu wa bungwe la FAM, Alfred Gunda wati ngati zitavute zisawakhudze.
"Ngati SULOM siyisintha masewerowa ndekuti atiderera nde kalikonse komwe kadzachitike kasadzatikhudze." Anatero Gunda.
Masewero amatimuwa amayenera kuchitikira ku bwalo la Bingu ngati kunali kutsatira mawu a FAM. Pakadali pano SULOM ikuonetsa kuti sikubwenza ganizo lawo lochititsa masewerowa pa bwaloli.
NAM ILI NDI MKUMANO WAUKULU
Bungwe loyendetsa mpira wa manja mdziko muno, la Netball Association of Malawi (NAM) lalengeza kuti mkumano wawo wawukulu wapachaka uliko lowerukali ku nyumba ya Civo ku Lilongwe kuyambira mmawa.
Bungwe lati mwazina, likasankha wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli pomwe a Chimwemwe Bakali anatula pansi udindo wawo chaka Chatha.
Iwo akaunikiranso mmene ndalama zayendera mu chaka cha 2022 mpaka 2023 komanso kusankha anthu ofufuza mmene ziziyendera mu ntchito za bungweli.
Noma vs NBB venue
Kamuzu Stadium
Goalkeepers
MARK HARISSON ALI PA MPENI
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Mark Harrison ali ndi tsogolo la pendapenda kutimuyi pomwe walephera kupambana mmasewero oyamba pa atatu omwe anapatsidwa kuti apambane.
Owinna ikudziwa zoti Harrison anapatsidwa masewero atatu amu Supa ligi kuti apambane atagonja mmasewero awo ndi Extreme FC. Mmasewero oyamba, Wanderers yafanana mphamvu ndi Dedza Dynamos 1-1 ndipo otsatira awiriwo akumane ndi FCB Nyasa Big Bullets ndi MAFCO.
Zinthu sizikuyenda kutimuku pomwe ochemerera atimuyi anayendetsa wapansi osewera ndipo ena anamenyedwa atatha masewero awo ndi Dedza Dynamos.
They must fire him quickly
Timu ya Mighty Wakawaka Tigers yatuluka mu chikho cha FDH Bank pomwe yagonja 3-1 ndi Santhe Admarc yomwe imasewera mu Chipiku Stores Central Region Premier Division.
Masewerowa anafika ku mapenate pomwe anathera 1-1 ndipo Precious Chipungu anagoletsa pa mphindi 29 ndipo Wellington Mkandawire anazigoletsera yekha mu golo lake.
Ku mapenate, goloboyi wa Santhe Admarc anachotsa ma penate awiri ndipo wati Tigers anachotsa limodzi kupangitsa Santhe kuti ipambane.
Iyo yakhala timu yachikhumi kuzigulira malo mu ndimeyi pomwe FCB Nyasa Big Bullets, Mighty Mukuru Wanderers, Silver Strikers, Extreme FC, Kamuzu Barracks, Moyale Barracks, MAFCO, Balaka FC ndi Bangwe All Stars afika pa ndimeyi.
Ayi anathera 3-1
MILANZIE WAPEREKA JERSEY KU KARONGA
Katswiri otchinga pagolo wakale ku Karonga United, Yonah Milanzie wapereka Jersey kutimu yake yakaleyi pofuna kuwathokoza pokhala naye bwino nthawi yomwe anali kutimuyi.
Wapampando wa timuyi, Alufeyo Chipanga watsimikiza za nkhaniyi ndipo wathokoza Milanzie kaya ka zomwe wachita.
Pakadali pano, Milanzie amasewera kutimu ya Mbeya Prison yaku Tanzania.