Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TITULUKANSO KU MBALI YA MATIMU OTULUKAWA" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Elvis Kafoteka, wati timu yake ikadali ndi mwayi waukulu kuti ituluke ku chigwa cha matimu omwe atuluke mu ligi pomwe wati mmasewero omwe akutsalira awiri awathandizire kutero.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 ndi timu ya Civil Service United pa bwalo la Mulanje Park lamulungu pomwe wati ndi zopweteka kwambiri kugonja timu ikusewera bwino.
Iye watinso timuyi anayipeza ili ku chigwa cha matimu otulukawa ndipo anayitulutsa ndipo panonso ayitulutsa.
"Ndinayipeza ili komweku kale ndipo panonso ndiyitulutsa bola tingochita bwino mmasewero athu ndi Baka City lachitatuli komanso ena otsatira zikatero zitikhalire bwino, timu ilibwino kale, ikusewera bwino koma tikumangopanga kavuto pang'ono." Anatero Kafoteka.
Mmasewero otsatira, timuyi ikumana ndi timu ya Baka City yomwe yatsimikizika kuti yatuluka mu ligi ndipo iwo ali pa nambala 14 ndi mapointsi 22 pa masewero 24 omwe yasewera.
📷: Civo
Mutumize pa 0991509953
"BULLETS INASEWERA BWINO KOMA MPIRA SUKUYENDA BWINO" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake yagonja chifukwa inakanika kuyigwira timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti isagoletse koyambilira komabe kayendetsedwe ka mpira sikali bwino mdziko muno.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Bingu ndipo wati anakonza kuti ayitchinge Bullets kuti isagoletse mu mphindi zoyambilira zenizeni koma zinavuta ndipo zinawabalalitsa.
Iye wati sakufuna kunamizira kugonjaku koma kusewera pafupifupi kukutopetsa osewera a timu yakeyi.
"Panopa zikuvuta chifukwa mpira tikusewera pafupifupi ndipo masiku 7 kusewera masewero atatu ndi zosagwira olo ku England sindikukhulupilira kuti zimachitika Izizi nde sikuti ndikunena kuti tagonja kamba ka izi koma zikufunika kuunikirapo." Anatero Kamanga.
Zateremu, timuyi tsopano yatuluka mu chikhochi ndipo FCB Nyasa Big Bullets yafika mu ndime yotsiriza ya chikhochi pomwe ikumane ndi Silver Strikers.
"ANALI MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati masewero omwe timu yake inasewera ndi FOMO anali ovuta poti anzawowa akufuna kuti atsalebe mu ligi koma mwamwayi apeza chipambano.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-2 ku bwalo la Mulanje Park ndipo wati chipambano chimenechi chawathandiza kwambiri kuti afike patali kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri, ndimadziwa kuti FOMO ibwera mwamphamvu chifukwa choti ikufuna itsalebe mu ligi nde tinavutika koma mwamwayi tapeza mipatayo tagwiritsa ntchito." Anatero Chidati.
Kutsatira kupambanaku, timuyi yafika pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 38 pa masewero 25 omwe yasewera chaka chino.
Photo: Civo media
"TIDZASANGALALA MASEWERO ONSE AKADZATHA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati timu yake idzasangalala masewero onse akadzatha kuti adzatsimikize kuti atsala mu ligi pomwe wati nthawi ino ndi yomenyera nkhondo kuti itsalebe mu ligiyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Moyale 1-0 pa bwalo la Balaka lamulungu ndipo wati timu yake inali ndi masewero ovuta poti Moyale Barracks ndi timu yabwino.
Iye wauzanso ochemerera atimuyi kuti chipambanochi ndi chiyambi cha zinthu zabwino kutimuyi ndipo ayesetsa kuti zikhale bwino.
"Mmene ligi yafikiramu zikufunika kuti tizipambana masewero nde sitisangaliratu koma tidikira kuti masewero onse athe kenako tidzasangalale chatsala ndi kulimbikira kuti tizichita bwino." Anatero Kajawa.
Timuyi ili pa nambala 13 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 24 pa masewero 26 omwe yasewera chaka chino.
"KULUZA MASEWERO NDI ZAMPIRA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake inayesetsa kuti ichite bwino ndipo inakonza kuti ipambane mmasewero awo koma sizinayende ndi momwe anakonzera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Bangwe All Stars lamulungu pa bwalo la Balaka ndipo wati timu yake inapeza mipata yochuluka kwambiri yomwe anakanika kugoletsa.
"Anali masewero abwino kwambiri tinapeza mipata kuti mwina tikanatha kupeza zigoli koma tinakanika komabe zimachitika mu mpira tibwerera tikakonze mavuto athu kuti tipitilire kuchita bwino." Anatero Mwansa.
Moyale Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi okwana 36 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Maxwell