SILVER ITHA KUPITIRA MU CASTEL
Timu ya Silver Strikers ikhonza kubwerera mu chikho cha Castel Challenge pomwe yalembera bungwe la Football Association of Malawi kuti timu ya Panthers inagwiritsa ntchito osewera omwe sanali oyenerera kusewerera timuyi.
Malingana ndi zomwe Owinna yawona, FAM yalandira kalata kuchokera ku Silver Strikers ndipo iyamba kufufuza Panthers yomwe ngati ipezeke olakwa itha kutuluka mu mpikisanowu.
Panthers inalowetsa osewera wakale wa Mzuni FC, Taniel Mhango, yemwe anasewerako mpikisano ngati omwewu ndi timu ya Ekwendeni United pomwe inkakumana ndi Malidade FC pa 30 June 2024 pomwe Aggrey Msowoya anasewerapo Mhuju FC yaku Rumphi.
Kutengera malamulo a mpikisanowu, osewera akuyenera kungosewerera timu imodzi yokha ndipo ngati asintha timu sali ololezedwa kuseweretsedwa.
Ndipo timu ya Panthers yati sinafikilidwe ndi timu ya Panthers kufunsidwa za nkhaniyi.
Source: Nation
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores