NKHANI
Mphunzitsi yemwe wachotsedwa kutimu ya Flames, Patrick Mabedi, wamupeza woyimira milandu wodziwika bwino, David Kanyenda, kuti amuthandizire pa milandu ya kuchotsedwa ntchito kwake kutimuyi.
Izi zadza pomwe bungwe la Football Association of Malawi linati silimupatsa kalikonse Mabedi kamba koti ndi zomwe zinali mu mgwirizano wawo kuti ngati sadzapita ku African Cup of Nations adzachoka.
Ndipo Kanyenda wanenetsa kuti ngati samupatsa ndalama zake komanso maphindu ena omwe akanawapeza, iwo akupita ku bwalo la milandu.
Source: Nation
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores