"TILIMBIKITSA ANYAMATA KU LIGI NDI CASTEL" - MPINGANJIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Bob Mpinganjira, wati anyamata ake amaoneka okhumudwa kwambiri kamba koti akuchokera kogonja koma awalimbikitsa kuti achite bwino ku ligi komanso mu chikho cha Castel.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Chipoka FC 10-1 pa bwalo la Kamuzu masana a lachiwiri ndipo wati timu yake inachita kuzitolera mchigawo chachiwiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri, tinayamba movutika chifukwa timachokera kogonja nde anyamata anali okhumudwa komanso molalo inali yotsika koma mchigawo chachiwiri tinakhazikika ndipo tinachita bwino." Anatero Mpinganjira.
Iye anati timu yake tsopano iyike chidwi chachikulu ku mpikisano wa chikho cha Castel komanso ligi ya TNM pomwe atuluka mu mpikisano wa Airtel Top 8.
Zateremu Manoma afika mu ndime ya matimu khumi, asanu ndi imodzi (16) a mpikisano wa Castel ndipo mayere achitika kuti adziwe yemwe akumane naye.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores