Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Simama
What have they considered between moyale and blue eagles?
Logtable
HJHJJHJ
NBB 2:1 silver
Man city 2:1 totenham
Bullets 1:1 silver
I have won it
Psd w
bb 2 bankers 1
"BLUE EAGLES NDI MAFCO ILI NGATI NDIME YOTSIRIZA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyembekeza kuti masewero awo ndi timu ya MAFCO lamulungu pa bwalo la Nankhaka akhale ovuta kwambiri poti matimu onse ali ndi zolinga ndi masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pomaliza ligi ya chaka chino ndipo wati akufunitsitsa kupambana ndi cholinga choti asewere nawo mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Airtel Top 8 a chaka cha mawa.
"Kukonzekera kwathu kwayenda bwino ndipo tachilimika chifukwa tikukakumana ndi MAFCO yomwe timavutitsana nayo nde masewero ake akhala ngati a ndime yotsiriza komabe kusewera kwake ndi komwe taonetsa kumapetoku, kungoika mtima kuti chaka cha mawa tidzasewere mu Airtel Top 8." Anatero Kananji.
Timuyi ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 ndipo kupambana ndi MAFCO kutha kudzawatengera pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7).
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
HARRISON WORRIED WITH KAMANGA'S 'SERIOUS' INJURY
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says he is worried with Mphatso Kamanga's current injury and that the doctors will fight to get him fit before the next year's league.
The British said this on Saturday ahead of the team's final match in the league against Civo United on Sunday and said Kamanga's injury is a blow as he has spent much of the season on the sidelines.
"Yah we have Isaac [Kaliati] who is injured and also Mphatso [Kamanga] has now a serious injury yesterday at training, I'm getting worried because he was injured and came back, he was performing well, last week he was a man of the match but now he gets injured at training I'm worried but the doctors will take him to hospital so that we have him before the start of next season." Said Harrison.
Ahead of the match, Harrison said his team will fight to finish on high as the match between Bullets and Silver Strikers can gift them the second position. The Nomads
"WE CANT WIN THE LEAGUE BUT FINISH SECOND" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says his team will look to claim maximum points on the final day so that they can finish on position two in the league.
He said this on Saturday ahead of their meeting with Civo United at the Civo Stadium on Sunday and said poor pitch and Civo's relegation threats are the main reasons why the match will be a tough one.
"It's not going to be any easy game obviously looking at the field is a mess it's not easy to play football on this artificial, it's just like that one in Mzuzu but anyway not only that, they are fighting for relegation so they have to win a point to give themselves a safety they cant rely on teams to drop points so they gonna fight for points tomorrow that's for sure." Said Harrison.
He further said it is important that the Nomads finish second in the league and has asked the supporters to go in numbers and chill the team.
"It's also important that we finish on
"CHAKA CHINO ANTHU AMBIRI SANATIPATSE MPATA" - SAMBANI
Mtsogoleri wa osewera ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Precious Sambani, wati ligi ya chaka chino yakhala ya mtengo wapatali ndipo wati ndi chaka chimene osewera alimbikira kwambiri poti mpira unavuta.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Silver Strikers pa Kamuzu mu masewero olimbirana ukatswiri wa ligi ndipo wati akudziwa kuti nkhondo siyinathe koma alimbikira kuti akapambane.
"Tikuwatenga ngati masewero aliwonse omwe mwina tikufanana mapointsi nde tikufuna ifeyo titsogole, nkhondo ilipo poti Silver ikungofunikira zigoli zinayi koma ifeyo tiyesetsa kuti tikapambane." Anatero Sambani.
Iye wati mgwirizano wa osewera komanso kulimbikitsidwa ndi aphunzitsi atimuyi kwathandiza osewerawa kuti alimbikire mpaka ali pa nambala yoyamba pano. Timuyi ikungofuna point imodzi kapena isakagonje ndi zigoli zodutsa zitatu kuti itenge ligi ya TNM.
"IT'S THE DAY MOST PLAYERS HAVE BEEN WAITING FOR" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says he expects a tough match against a Silver Strikers side that are eager to win the TNM Super league but says it is in the hands of his players to finish up the job on Sunday.
He said this ahead of his team's final match of the season and said most of his players have been waiting for this day to win the tournament meaning they will fight for it.
"I think in the game the boys know how they came, how it felt to get how we are today and I think to most of the guys in the team have been waiting for this game and interms of motivation wise, it's up to the players to raise their heads up and go up and finish the race." Said Pasuwa.
He said the league has been tough on them as they have been travelling a lot so they will try to make supporters to enjoy Football against Silver. He said Silver is a good side but they will fight.
"It will be interesting we are playing a team th
LUNGU MISSES THE SILVER MATCH
FCB Nyasa Big Bullets will not have their left back, Alick Lungu, in their final match of the season against Silver Strikers on Sunday due to injury.
The team's head coach, Callisto Pasuwa, confirmed about the news on Saturday ahead of match and said he has joined Rabson Chiyenda and Frank Willard on the sidelines.
Lungu has missed many games this season due to injury and came back in the team in their goalless draw against Blue Eagles two weeks ago.
TEMWA WINS FOURTH GOLDEN BOOT IN 2023
Scorchers forward, Temwa Chawinga, has won his fourth golden boot award of the year 2023 after netting 30 goals in 22 games to help Wuhan Jiangda win the 2023 China Women's Super League on Saturday.
Temwa netted a hat trick against Zhejiang Hangzhou as Wuhan won 5-1 in the final match of the season to claim the award ahead of Zambia's Barbra Banda of Shanghai who has netted 16 goals this season.
Wuhan have finished the league with 61 points from their 22 games as they have dropped only 5 points this season and the golden boot its Temwa's third for the club only this year.
She won the golden boot also in China Super Cup and the China Football Association Cup plus a COSAFA Women's Championship golden boot award with the Scorchers.
Reporter: Hastings Wadza Kasonga Jr
When could silver meet wanderers
"KB IMATITENGA NGATI AZIKAZAWO NDE TINATOPA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inakonzeka bwino kwambiri patsogolo pa masewero awo ndi Kamuzu Barracks ndipo anayeneradi kuti apambane.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa KB 3-1 pa bwalo la Civo lachinayi ndipo wati timuyi inatopa kugonja ndi timuyi ndipo apa inabwera ndi mtima wonse kuti ipambane.
"Tithokoze Mulungu komanso tithokoze anyamata athu kamba koti tachita bwino, KB imatitenga ngati azikazi awo tikakumana amangotimenya koma apa tinangoti mmene tinamenyera ndi Bullets tikapite chomwecho nde tinakonzekadi ndipo anyamata achita kunenadi kuti tawathamangitsa." Anatero Kananji.
Blue Eagles yakhala timu yachisanu ndi chiwiri (7) kuti ifike mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Castel Challenge Cup ndipo idzakumana ndi timu ya Silver Strikers mu ndimeyi.
"MWINA SITIMATHA KUSIYANITSA ZIKHO ZINA NDI LIGI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati timu yake yakanika kuchita bwino mu zikho zina za mdziko muno kusiyana ndi ligi chifukwa choti masewero onse amawasewera mofanana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 ndi Blue Eagles lachinayi kuti atuluke mu chikho cha Castel Challenge Cup ndipo iye anati timuyi sinasewere bwino ndipo imayeneradi kugonja ndi kaseweredwe kameneko.
Iye wati timuyi yavutika kuti ichite bwino mu zikho zina monga FDH Bank, Airtel Top 8 komanso cha Castel kamba ka kaganizidwe ka mmene azisewerera masewerowa.
"Ndi zoona kuti tavutikadi mma cup bolako mu ligi mwina chifukwa cha kaganizidwe chifukwa amu zikho zinazi timasewera kuti zithere pomwepo pomwe mu ligi kufanana mphamvu mmasewero enawo timadzapambana nde kusasiyanitsaku ndi komwe kwatipweteketsa." Anatero Kalinda.
Timu ya KB ili pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM ndi mapointsi 45 pa masewero 29 omwe yasewer
1-2
LOGTABLE
Top geals
Top goasl
Now
Fcb nyasa big bullet vs kalonga united FC
"DON'T MISINTERPRET MY ACTIONS, I'M NOT AFRAID" - NYAMILANDU
Football Association of Malawi President, Walter Nyamilandu Manda, says his decision to appeal against the candidature of his opponent, Fleetwood Haiya, should not be taken as a sign of fear and weakness.
He said this after his appeal to the FAM electoral body that Haiya should not be allowed to start because he has not resigned from his position as Super League of Malawi's President was denied for a late submission.
He said he is more than ready to defend his position and that he was just promoting justice and the laws of the country.
"My actions to appeal should not be misinterpreted as a sign of weakness but rather a gesture of boldness to stand for justice against the oppressed and to defend the statuses that govern Malawi Football." Said Nyamilandu to Nation Newspaper.
Nyamilandu has been in charge since 2004 at the mother body in the country and got 3 nominations to Haiya's 5 nominations ahead of December 16 Electi
"MALAMULO AKUNENAWO NDE SITIKUWADZIWA" - HUMBA
Mtsogoleri wa bungwe loyendetsa mpira kummwera kwa dziko kuno la Southern Region Football Association, Raphael Humba, wati sakudziwa zoti kuli ndondomeko ya kasankhidwe ka anthu opita ku chisankho cha FAM ndipo ngati zilipo apatsidwe kuti awone.
Iye wayankhula izi poyankhapo pa nkhani yoti bungwe loona za ziphuphu ndi katangale mdziko muno likumufufuza kamba kosokoneza malamulo pofuna kusankha anthu okavota. Iye wati amatsatira malamulo a bungweli.
"Akukamba za ma by-laws omwe ifeyo sitikuwadziwa ndipo ku bungwe lathu kulibe moti tiwapempha kuti atipatseko tiwawone koma ntchito yosankha anthu kuti akatiyimilire ku FAM pa chilichonse amasankha ndi chair nde malamulo enawo sinkuwadziwa." Anatero Humba.
Bungwe la Malawi National Council of Sports lauza FAM kuti ilembe lipoti yokhudza mmene anthu ovota amasankhidwira ku bungweku ndi zomwe ankakambirana pa mikumano ya SRFL mu zaka za mmbuyomu.
ACB YALANDIRA NKHANI YOTI HUMBA AMAKAKAMIZA ANTHU KUVOTERA NYAMILANDU
Bungwe la Malawi National Council of Sports lalembera bungwe la Football Association of Malawi kuti Anti-Corruption Bureau lalandira dandaulo loti mtsogoleri wa Southern Region Football Association, Raphael Humba, amasokoneza malamulo kuti anthu avotere Walter Nyamilandu Manda.
Mu kalata imene Sports Torch yalowa usiku wapitawu yati kukakhala msonkhano waukulu ku FAM, mabungwe akumpoto, pakati ndi kummwera amakhala ndi mkumano wawukulu ndipo kulikonse kumachokera anthu asanu ndi mmodzi (6).
Pa anthuwa, atsogoleri, msungichuma ndi alembi amayenera apezekeko pomwe enawo amachita kusankhidwa mwa chisankhesankhe malinga ndi lamulo. Zamveka kuti a Humba amasankha okha anthu opita ku msonkhanowu omwe akuoneka kuti angasankhe Walter.
MNCS yauza FAM kuti itumize malamulo a bungwe la SRFA komanso mmene ankasankhira anthu ndi zomwe ankakambirana pa mikumano ya mmbuyomu ku bungweli pasanakwane pa 01 December 2023. Humba aku
0-3
"KARONGA IMAVUTA KWAMBIRI PAKWAWO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati akuyembekeza kuti masewero atimu yawo ndi Karonga United akhala ovuta poti Karongayi imavuta pakwawo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Karonga ndipo wati anyamata ake akudziwa kufunikira kopeza chipambano mmasewerowa ndikuti atenge ukatswiri wa ligi.
"Tikuyembekeza kuti akhala masewero ovuta kwambiri chifukwa Karonga ikakhala pakwawo imavuta komabe tawauza anyamata kufunikira kwa masewerowa ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti pakutha pa masewerowa tidzakhala mbali yopambana." Anatero Munthali.
Mapale ali pa nambala yoyamba mu ligiyi ndi mapointsi 56 pa masewero 28 omwe yamenya ndipo ngati ingagonjetse Karonga itenga ukatswiri wa ligi ya TNM.
"TILIBE PHUMA LILILONSE KOMA BULLETS ILI NALO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake ilibe phuma lililonse patsogolo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ligi ya TNM koma wati Bullets ndi yomwe ili ndi phuma kuti iwine.
Kajawa amayankhula patsogolo pa masewero awo pa bwalo la Karonga lachitatu ndipo wati anyamata ake akudziwa kufunikira kopambana masewerowa kuti athere mu matimu asanu ndi atatu oyamba.
"Tilibe phuma lililonse mwina tikanakhala ndi phuma tikanati mwina tili poti tituluka koma anzathuwa nde ali ndi phuma chifukwa akufuna kutenga ligi nde ifeyo takonzekera, sitimagonjagonja pakhomo nde tionetsetsa kusunga mbiri imeneyi kuti tichite bwino tithere mu Top 8." Anatero Kajawa.
Atakumana mchigawo choyamba, Bullets inapambana 2-0 ku Blantyre. Karonga ili pa nambala 8 ndi mapointsi 37 pa masewero 28 omwe yasewera mu ligiyi.
CHAWANANGWA ABWERERA PA BWALO POSACHEDWA
Katswiri wa timu ya Flames komanso ZANACO, Chawanangwa Kaonga, watsala pang'ono kubwereranso mu bwalo la zamasewero pomwe wayamba zokonzekera zomuthandiza kuti azitolere kuchokera ku kuvulala kwake.
Mmodzi mwa anthu omwe amayang'ana za physiotherapy ku timu ya Zanaco, Emmanuel Chimpango, watsimikiza kuti katswiriyu wayamba zokonzekeranzi kuti awongole minyewa cholinga choti achire bwinobwino.
"Chawanangwa tinamuyeza kachikena kuti tione ngati akuchira bwinobwino nde zotsatira zinayenda bwino, wachira mwina 90% aponso mutha kuona kuti aakuziongola cholinga choti akonzekeretse minyewa yomwe inavulala kuzolowera kugwiranso ntchito." Anatero mu chingerezi ndi olemba nkhani a timuyi.
Chawanangwa anavulala mmasewero omwe Malawi inkasewera ndi Guinea mu mwezi iwiri yapitayo ndipo mu ligi yaku Zambia ali ndi zigoli ziwiri pa masewero atatu omwe wasewera.
JUST IN
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakanika kuchita zokonzekera zawo pa bwalo la Karonga masana a tsiku la lero kamba koti anthu ena anafika ndi kudzawachitira zosokoneza pa bwalopa.
Bullets ikumana ndi Karonga United mu masewero awo achi 29 mu ligi ya TNM.
Source: Nkhoma FM
POLOKWANE BANNED FOR NOT PAYING KHUDA
DSTV Premiership side, Polokwane City, have been handed a FIFA transfer ban until they pay their former player Khuda Muyaba.
This comes after the player dragged the team to the World governing body after being not paid leading him to terminate his contract with the team.
Muyaba recently played for Tishreen SC in Syria before parting ways with the team.
Source: SABC Sport
Long table
CHIGAMULO CHOYAMBA CHILIPO MAWA
Chigamulo choyamba chenicheni choti anthu adziwe kuti ligi ilowera kuti chiliko lachitatu pa 29 Novembala 2023 pomwe omwe akutsogolera ligiyi, FCB Nyasa Big Bullets, akukumana ndi Karonga United pa bwalo la Karonga mu ligi.
Matimuwa ndi okha omwe atsala ndi masewero 28 mu ligi ndipo zotsatira za pa masewero amenewa zili ndi matanthauzo osiyanasiyana malingana ndi mmene zidzayendere mu tsiku lomaliza la ligiyi.
Ngati Bullets itapambane ndi Karonga ndekuti timuyi ikhala akatswiri a ligi ya TNM ya 2023 ndipo ngati atalepherane ndi kukhala pa mapointsi 57 ndekuti Silver Strikers ili ndi mwayi wotenganso chikhochi koma Wanderers ayi.
Ngati Bullets ingagonje ndi Karonga ndekuti matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers ali ndi mwayi waukulu kuti atha kudzatenga chikhochi lamulungu likudzali.
Bullets ili pa nambala yoyamba ndi mapointsi 56 pa masewero 28 pomwe Karonga ili ndi mapointsi 37 pa masewero 28 pa nambala yachisanu ndi chitatu.
0-2
FAM YAKANA PEMPHO LA NYAMILANDU LOCHOTSA HAIYA
Bungwe la Football Association of Malawi kudzera mu komiti yoyang'ana za chisankho cha bungweli lakana pempho la mtsogoleri wa FAM loti Haiya achotsedwe pa ndandanda wa anthu oyimira chisankho poti sanatule pansi maudindo ake.
Komitiyi yati a Nyamilandu asemphana ndi zomwe bungweli linanena litatulutsa mayina kuti dandaulo lililonse litumizidwe pasanathe masiku atatu.
Iwo anatulutsa mayina pa 18 November 2023 pomwe a Nyamilandu ndi oyimira pa mlandu awo alemba pa 24 November ndipo mlanduwu auchotsa kuti ndi wosamveka poti sungasinthitse malamulo a komitiyi.
"SALIMA NDI WOSEWERA WAPAMWAMBA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wayamikira wosewera watimu yake, Chikumbutso Salima, kuti ndi katswiri wodziwa mpira ndipo ali ndi tsogolo lowala mu mpira wake.
Iye amayankhula katswiriyu atagoletsa zigoli ziwiri mmasewero omwe timuyi inalepherana 2-2 ndi timu ya Civo loweruka lathali ndipo anati Salima wosewera wapamwamba.
"Uyuyu ndi katswiri, zigoli zapamwamba kwambiri ndipo ndi wosewera yemwe watithandiza kwambiri. Luso lake la katswiriyu lidzamutengera patali kwambiri." Anatero Mkandawire.
Katswiriyu wakwanitsa kugoletsa zigoli zisanu ndi zitatu (8) angakhale kuti anakhala masabata angapo asakusewera mpira kamba kovulala. Salima anachokera ku FCB Nyasa Big Bullets kupita ku timuyi pa ngongole.