"TILIBE PHUMA LILILONSE KOMA BULLETS ILI NALO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake ilibe phuma lililonse patsogolo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ligi ya TNM koma wati Bullets ndi yomwe ili ndi phuma kuti iwine.
Kajawa amayankhula patsogolo pa masewero awo pa bwalo la Karonga lachitatu ndipo wati anyamata ake akudziwa kufunikira kopambana masewerowa kuti athere mu matimu asanu ndi atatu oyamba.
"Tilibe phuma lililonse mwina tikanakhala ndi phuma tikanati mwina tili poti tituluka koma anzathuwa nde ali ndi phuma chifukwa akufuna kutenga ligi nde ifeyo takonzekera, sitimagonjagonja pakhomo nde tionetsetsa kusunga mbiri imeneyi kuti tichite bwino tithere mu Top 8." Anatero Kajawa.
Atakumana mchigawo choyamba, Bullets inapambana 2-0 ku Blantyre. Karonga ili pa nambala 8 ndi mapointsi 37 pa masewero 28 omwe yasewera mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores