"BLUE EAGLES NDI MAFCO ILI NGATI NDIME YOTSIRIZA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyembekeza kuti masewero awo ndi timu ya MAFCO lamulungu pa bwalo la Nankhaka akhale ovuta kwambiri poti matimu onse ali ndi zolinga ndi masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pomaliza ligi ya chaka chino ndipo wati akufunitsitsa kupambana ndi cholinga choti asewere nawo mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Airtel Top 8 a chaka cha mawa.
"Kukonzekera kwathu kwayenda bwino ndipo tachilimika chifukwa tikukakumana ndi MAFCO yomwe timavutitsana nayo nde masewero ake akhala ngati a ndime yotsiriza komabe kusewera kwake ndi komwe taonetsa kumapetoku, kungoika mtima kuti chaka cha mawa tidzasewere mu Airtel Top 8." Anatero Kananji.
Timuyi ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 ndipo kupambana ndi MAFCO kutha kudzawatengera pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7).
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores