"SALIMA NDI WOSEWERA WAPAMWAMBA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wayamikira wosewera watimu yake, Chikumbutso Salima, kuti ndi katswiri wodziwa mpira ndipo ali ndi tsogolo lowala mu mpira wake.
Iye amayankhula katswiriyu atagoletsa zigoli ziwiri mmasewero omwe timuyi inalepherana 2-2 ndi timu ya Civo loweruka lathali ndipo anati Salima wosewera wapamwamba.
"Uyuyu ndi katswiri, zigoli zapamwamba kwambiri ndipo ndi wosewera yemwe watithandiza kwambiri. Luso lake la katswiriyu lidzamutengera patali kwambiri." Anatero Mkandawire.
Katswiriyu wakwanitsa kugoletsa zigoli zisanu ndi zitatu (8) angakhale kuti anakhala masabata angapo asakusewera mpira kamba kovulala. Salima anachokera ku FCB Nyasa Big Bullets kupita ku timuyi pa ngongole.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores