CHAWANANGWA ABWERERA PA BWALO POSACHEDWA
Katswiri wa timu ya Flames komanso ZANACO, Chawanangwa Kaonga, watsala pang'ono kubwereranso mu bwalo la zamasewero pomwe wayamba zokonzekera zomuthandiza kuti azitolere kuchokera ku kuvulala kwake.
Mmodzi mwa anthu omwe amayang'ana za physiotherapy ku timu ya Zanaco, Emmanuel Chimpango, watsimikiza kuti katswiriyu wayamba zokonzekeranzi kuti awongole minyewa cholinga choti achire bwinobwino.
"Chawanangwa tinamuyeza kachikena kuti tione ngati akuchira bwinobwino nde zotsatira zinayenda bwino, wachira mwina 90% aponso mutha kuona kuti aakuziongola cholinga choti akonzekeretse minyewa yomwe inavulala kuzolowera kugwiranso ntchito." Anatero mu chingerezi ndi olemba nkhani a timuyi.
Chawanangwa anavulala mmasewero omwe Malawi inkasewera ndi Guinea mu mwezi iwiri yapitayo ndipo mu ligi yaku Zambia ali ndi zigoli ziwiri pa masewero atatu omwe wasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores