FAM YAKANA PEMPHO LA NYAMILANDU LOCHOTSA HAIYA
Bungwe la Football Association of Malawi kudzera mu komiti yoyang'ana za chisankho cha bungweli lakana pempho la mtsogoleri wa FAM loti Haiya achotsedwe pa ndandanda wa anthu oyimira chisankho poti sanatule pansi maudindo ake.
Komitiyi yati a Nyamilandu asemphana ndi zomwe bungweli linanena litatulutsa mayina kuti dandaulo lililonse litumizidwe pasanathe masiku atatu.
Iwo anatulutsa mayina pa 18 November 2023 pomwe a Nyamilandu ndi oyimira pa mlandu awo alemba pa 24 November ndipo mlanduwu auchotsa kuti ndi wosamveka poti sungasinthitse malamulo a komitiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores