"KARONGA IMAVUTA KWAMBIRI PAKWAWO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati akuyembekeza kuti masewero atimu yawo ndi Karonga United akhala ovuta poti Karongayi imavuta pakwawo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Karonga ndipo wati anyamata ake akudziwa kufunikira kopeza chipambano mmasewerowa ndikuti atenge ukatswiri wa ligi.
"Tikuyembekeza kuti akhala masewero ovuta kwambiri chifukwa Karonga ikakhala pakwawo imavuta komabe tawauza anyamata kufunikira kwa masewerowa ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti pakutha pa masewerowa tidzakhala mbali yopambana." Anatero Munthali.
Mapale ali pa nambala yoyamba mu ligiyi ndi mapointsi 56 pa masewero 28 omwe yamenya ndipo ngati ingagonjetse Karonga itenga ukatswiri wa ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores