ASCENT ACADEMY YAPAMBANA 8-0 KU ICELAND
Timu ya Ascent Academy yomwe ili mdziko la Iceland, yayamba masewero a chikho cha Rey Cup mwapamwamba pomwe yagonjetsa Reykjavik yaku Iceland 8-0 lachinayi.
Katswiri wa timuyi, Mwiso Mhango, anagoletsa zigoli zitatu yekha pomwe Lameck Mithi, James Chibala, Yusuf Nathunga, Hermas Masinja komanso Blessings Lungu anamwetsa chigoli chimodzi aliyense kuti apambane masewerowa.
Wamkulu wa watimuyi, Thom Nkolongo, anali wosangalala ndi mmene osewera achisodzerawa anachitira mmasewero awo malingana ndi kupeza kwa Owinna.
"Maseweredwe mu masewero oyamba anali bwino kwambiri ndipo zinali zosangalatsa kuona osewera asewera mwapamwamba motere. Anyamata amasewera ndi mpira kuusunga ndi kupanga nawo chilichonse, asewera bwino ndithu." Anatero Nkolongo.
Mdzikomo, timuyi yasewerakonso masewero apaubale pomwe inapha UMFA 5-0 chipitireni kumeneko. Iyo ikumana ndi matimu enanso aku England ndi Germany mu mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores