"OSEWERA ASAMASANKHE MALO" - WISDOM
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Wisdom Mpinganjira, wati iye anangochikhazikitsa kuti asewere pa malo omwe mphunzitsi watimuyi angafune kuti amuseweretse pomwe wasewera mmalo odutsa asanu mu ligi ya chaka chino.
Mpinganjira amayankhula izi atatha masewero a timuyi ndi Blue Eagles omwe anapambana 1-0 ndipo anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa ena. Iye anati akumalimbikira komanso kupanga zomwe mphunzitsi akufuna ndi pomwe akufuna kusewera.
"Ndinangochikhazikitsa kuti ndimenye pomwe coach akufuna, osewera samasankha malo nde ineyo ndimagwira ntchito basi."
Katswiriyu wasewerapo ngati wotchinga kumbuyo wa kumanja, kumanzere, osewera mmbali yakumanja ndi kumanzere komanso osewera kutsogolo cha mmbali mu masewero 13 omwe wasewera chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores