"TIKAWAPHUNZITSE OSEWERA KUMWETSA ZIGOLI BASI" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyenera kukawaphunzitsa osewera ake akutsogolo kuti azimwetsa zigoli pomwe wati timu yake ikutaya mipata yochuluka.
Kananji amayankhula izi atatha masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers omwe anagonja 1-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira osewera ake kuti anasewera bwino koma wati mipata yochuluka ikungotayika.
"Tikuyenera kuti tibwerere kuti tikakonze ndi kuwaphunzira osewera athu akutsogolo kuti azimwetsa zigoli, kusewera nde tikuchita bwino koma mipata nde tikuyitaya yambiri, tikudutsa mu nyengo yowawa kuti ziyamba kuyenda." Kananji anatero.
Timu ya Blue Eagles yagonja masewero asanu ndi imodzi otsogozana mu zikho zonse pomwenso yatuluka mu chikho cha FDH sabata yatha. Timuyi ili pa nambala 12 ndi mapointsi 15 pa masewero 14 ndipo amaliza chigawo choyamba pokumana ndi Mighty Wakawaka Tigers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores