BALIKINHO WASEWERA MASEWERO KU WANDERERS
Katswiri yemwe anathawa ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers chaka Chatha, Balikinho Mwakanyongo, wasewera masewero ake oyamba mu chaka chino ndi timuyi pomwe anachokera panja mmasewero omwe timuyi yagonjetsa Blue Eagles 1-0 lamulungu.
Balikinho analowa pomwe chigawo chachiwiri chimayamba ndipo anasinthana ndi Francis Mkonda. Iye anasewera ngati wapakati wopita kutsogolo osati motchinga ngati mmene amadziwikira.
Iye ànasintha zinthu pakati pa timuyi pomwe kulowa kwake, Wanderers inapeza chigoli cha masewerowa. Patatha mphindi 56, iye analandira kalata yachikasu kamba kosamufikira bwino Gilbert Chirwa.
Masewero otsatira omwe atha kusewera ndi pakati pa timuyi ndi MAFCO pa bwalo la Chitowe mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores