Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"PANO TSOPANO NDE TANYAMUKA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati tsopano timuyi yanyamuka mu ligi ya chaka cha 2024 pomwe tsopano apeza chipambano chawo choyamba.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-1 ndi timu ya FOMO ndipo wati chipsmbanochi chafika mu nthawi yake pomwe chiwapatse mphamvu kuti ayende bwino mu ligiyi.
"Kupambana kwalero kutipatsa mphamvu zochuluka chifukwa ndekuti chitsogolo chizioneka bwino kwambiri komanso tsopano tanyamuka chifukwa zikweza molalo pakati pa anyamata athu." Anatero Kamanga.
Timu ya Kamuzu Barracks tsopano yakwanitsa kutenga ma points asanu pomwe ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi mu ligiyi.
SUPER SAKUWA PATNERS KB
TNM Super League 2016 season Champions, Kamuzu Barracks, has revealed Super Sakuwa Steel Limited as their official partner for the ongoing 2024 soccer season.
The announcement has been made on Friday as the two sides have made an agreement that the company will sponsor the team's kit for the 2024 season with the team's logo.
The deal also include a K100,000 prize to any player who wins a player of the month and K50,000 for the man of the match winners.
Last season, the Yellow Marines were sponsored by Masters Bakery Company but the deal ended after the end of the season.
"OYIMBIRA WALERO SAMATHA KUIMBIRA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, walavulira khala la Moto kwa oyimbira, Lameck Manda, kuti samatha kugwira ntchito poti ziganizo zimamuvuta kupanga.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi MAFCO pa Chitowe ndipo ziganizo za oyimbira sizinali zabwino Kwa iwo.
"Oyimbira masewero awawa sanatikonde ndipo uyuyu samatha kuimbira, tinabweraponso pano anawononga masewero nde tisamayesane ngati olephera chifukwa timagwira ntchito kukonzekera basi nkumabwera kudzaononga zinthu, sindikuti MAFCO yachinya chigoli cholakwika koma samadziwa ziganizo." Anatero Kamanga.
Kamuzu Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi awiri pa masewero awirinso omwe yasewera.
"ZIKANAKHALANSO ZIGOLI ZITATU" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake imayenera kupambana poti yaphonya mipata yabwino koma wakondwera ndi mmene zotsatira zayendera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi Mighty Mukuru Wanderers ku Blantyre ndipo wati ndi okhutira ndi zotsatirazi.
"Ndine wokondwa kwambiri poti zayendera chonchi, moyenda kupeza point imodzi ndekuti zilibwino koma mwina tikanatha kupeza zigoli zitatu koma takanika kugwiritsa ntchito mipata yathu koma tikakonza zonse tikabwerera kunyumba." Anatero Kamanga.
Timuyi tsopano ili ndi point imodzi atasewera masewero amodzi ndipo yakhala pa nambala yachisanu ndi chinayi mu ligiyi.
Photo: Wanderers media
KB BEATS MAFCO IN A FRIENDLY
The new 2024 season is here and Kamuzu Barracks' preparations for the new season have started on high after beating MAFCO 3-2 in a Friendly.
Zinjani Yonah scored two goals with Sheriff Maulana netting the other for KB while Mphatso Philimoni and an own goal from Gilbert Nkhokwe got two for MAFCO.
This is the first friendly match for both soldiers as they aim to have a successful season.
KB SELECT 19 OUT OF 80
Kamuzu Barracks Football Club has announced that it will unveil 19 players that have been selected from the trials that were successful in the trials they conducted from 5 to 9 February 2024.
The team confirmed the news on Friday via their Facebook page that 61 players from 80 that attended the trials failed to impress the Alick Chirwa led panel.
Meanwhile, Chirwa said the process was good and have settled for the best players.
"The trials were successful, we have spotted the talents we were missing, there is competition in all departments now," commented Chirwa.
He further said that they will start training with the rest of the team on Monday in order to blend old and new players together.
Last season, the Soldiers finished fifth with 46 points from 30 games.
"MU ZAKA ZIKUBWERAZI TIDZAKHALANSO PAMWAMBA" - KAWANGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Blessings Kawanga, wati timu yake sikuti yachita bwino kwambiri poti yatsika pa ndandanda poyerekeza ndi chaka Chatha koma wati kutsogoloku adzatheranso kumtundako.
Kawanga amayankhula atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers ndipo wati ndi zokhumudwitsa kuti mulingo womwe anapatsidwa ndi akuluakulu sanakwanitse komabe kutsogoloku ziyenda.
"Ndi zokhumudwitsa kuti chaka chinonso tilibe choti tiloze pa tebulo komabe zaka zikudzazi tiyesetsa kutero kuti mwina tibwererenso ngati zaka zammbuyomu kungoti mpira ndi wovuta poti umapanga zinthu zosiyana ndi zomwe tinakonza." Anatero Kawanga.
Timuyi tsopano yathera pa nambala yachisanu ndi mapointsi okwana 46 pa masewero omwe yasewera mu ligi ya chaka chimodzi. Aphunzitsi a timuyi anauzidwa kuti atengeko ka chikho kamodzi chaka chino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"MWINA SITIMATHA KUSIYANITSA ZIKHO ZINA NDI LIGI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati timu yake yakanika kuchita bwino mu zikho zina za mdziko muno kusiyana ndi ligi chifukwa choti masewero onse amawasewera mofanana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 ndi Blue Eagles lachinayi kuti atuluke mu chikho cha Castel Challenge Cup ndipo iye anati timuyi sinasewere bwino ndipo imayeneradi kugonja ndi kaseweredwe kameneko.
Iye wati timuyi yavutika kuti ichite bwino mu zikho zina monga FDH Bank, Airtel Top 8 komanso cha Castel kamba ka kaganizidwe ka mmene azisewerera masewerowa.
"Ndi zoona kuti tavutikadi mma cup bolako mu ligi mwina chifukwa cha kaganizidwe chifukwa amu zikho zinazi timasewera kuti zithere pomwepo pomwe mu ligi kufanana mphamvu mmasewero enawo timadzapambana nde kusasiyanitsaku ndi komwe kwatipweteketsa." Anatero Kalinda.
Timu ya KB ili pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM ndi mapointsi 45 pa masewero 29 omwe yasewer
"KUGONJA KWA LERO NDI KOPWETEKA KWAMBIRI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati timu yake yagonja mopweteka kwambiri pomwe wati point inali yabwino kwa iwo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 2-1 ndi Silver Strikers pa bwalo la Bingu lachinayi ndipo wati chigoli cha Chimwemwe Idana ndi chowawa kwambiri kumbali yawo.
"Ndi zoonadi tagonja masewerowa koma tagonja mopweteka kwambiri chifukwa kunali kutangotsala ma seconds moti kufanana mphamvu kunali kwabwino kwa ife komabe tingovomereza kuti zayenda motero koma zatipweteka kwambiri." Anatero Kalinda.
Iye anati timu yake iyesetsa kuti idzapambana mmasewero awo ndi Mighty Wakawaka Tigers kuti ilimbitse mwayi wawo othera pa nambala yaku mapeto. KB ili pa nambala yachinayi ndi mapointsi 45 pa masewero 29 omwe yasewera.
HOT!
Kamuzu Barracks forward, Olson Kanjira, was on target again for Kamuzu Barracks against Silver Strikers at the Civo Stadium on Thursday.
He has taken his tally to 10 in the league with 60 percent of the goals scored against the top four teams this season.
β’FCB Nyasa Big Bullets - 2 goals β’Mighty Mukuru Wanderers - 2 goals β’Silver Strikers - 1 goal β’Chitipa United - 1 goal
#KasongaJr
KB YASAMUTSA CHITIPA KU PLOT 4
Timu ya Kamuzu Barracks yalimbitsa mwayi wawo womaliza pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM pomwe yachotsa timu ya Kamuzu Barracks pa malopa atagonjetsa Extreme FC 1-0 pa bwalo la Civo lachitatu.
Sheriff Maulana anamwetsa chigoli chopambanira pa mphindi 89 zamasewerowa kuti KB ipeze mapointsi atatu zomwe wachiwiri kwa mphunzitsi wawo, Ted Kalinda anakondwera kwambiri.
"Tithokoze Mulungu kamba koti tapambana, masewero anativuta mchigawo choyamba poti anyamata anali ndi phuma kuti akapambana afika pa nambala yachinayi nde timangotaya mipira koma titawayankhula anakonza mpaka tinapeza chigoli." Anatero Kalinda.
Iye wati timuyi ichilimika kuti imalizire pa nambala yachinayiyi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 45 pa masewero 28 ndipo singakwanitse kutenga ligi kapena kufika pa nambala yachitatu.
"TIKUDABWA KUTI MPIRA WATHU UKUYENDA BWANJI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati wadabwa ndi uthenga woti timu yake yatuluka mu Airtel Top 8 chonsecho pa nkumano womwe unalipo masewero asanayambe anati akalepherana ifika ku mapenate.
Kalinda amayankhula izi atatha masewero omwe atuluka mu chikhochi angakhale kuti alepherana 1-1 ndi MAFCO ndipo wati chiganizo choti yochinya koyenda ipitilira chabwera kutangotsala mphindi zisanu.
"Ndikudabwa kuti akuti tatuluka malamulo azikhala mmene alili, ku mkumano masewero asanayambe anatikumbutsa kuti masewero kaya atha 1-1 kaya 0-0 afika ku mapenate koma kutatsala mphindi 5 ndi pomwe akuti zikatha chonchi MAFCO ipitilira." Anatero Kalinda.
Iye wati ngati kuli kukamang'ala pa nkhaniyi si mbali ya aphunzitsi a timuyi komatu akuluakulu a timuyi. Zateremu timuyi yatuluka mu chikhochi ndipo maso awo ayang'ana pa Castel Challenge Cup ndi TNM Supa ligi.
"TIKUFUNA TIKWERE MU LIGI" - CHIRWA.
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati masewero atimuyi ndi Red Lions anali ofunikira kwambiri pomwe akuyang'ana kuti athere pa nambala yabwino mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Red Lions 2-0 pa bwalo la Balaka ndipo wauza ochemerera atimuyi kuti iwo agwira ntchito yotamandika.
"Anali masewero ofunikira kwambiri kuti tikwere mu ligi nde 2-0 kupambana ndine okondwa kwambiri. Masapota akhalebe nafe, ife tiyesetsa kuti tigwire ntchito ndipo timaliza pa bwino ndithu." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks tsopano yasuzumira ku matimu anayi oyamba mu ligiyi pomwe ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 39 pa masewero 25 omwe yasewera.
#Tawonga2023
"TIKANAWINA KOMA OYIMBIRAWA SANAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, anachoka atakwiya pa bwalo la Mpira loweruka pomwe wati oyimbira amapanga ziganizo zofuna kuyipweteka timu yake pomwe imasewera ndi Bangwe All Stars.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe anafanana mphamvu 1-1 ndi zigoli za Levison Maganizo komanso James Tambwali ndipo wati kukonza kwawo kunali kuti apambane basi.
"Anali masewero ophweka kwambiri koma oyimbira amafuna kuti tizilimbana. Nokha mukuona chinthu akakukanirani molalo imatha nde timangokhala kumbuyo kuja poopa kuti awapatsa chigoli mwina cha offside." Anatero Chirwa.
Iye wati sanakhutire ndi zotsatirazi pomwe wati anakonza kuti apambane. KB ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 36 pa masewero 24.
"ANALI MANGAWA KUTI TIKUNTHE CHITIPA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati timu yale inali ndi mangawa aakulu pa timu ya Chitipa United kuti apambane mmasewero awo kutsatira kuti iwo anagonja atapita ku Karonga mchigawo choyamba.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yapambana 2-0 pa bwalo la Kasungu ndipo wati apa tsopano akhonza kulengezano kuti KB yabwerano.
"Lero tapambana 2-0 Tithokoze Mulungu, kupambana kwa lero anali mangawa chifukwa anatimenya mchigawo choyamba pakwawo nde tinakonza kuti mchigawo choyamba tichinye zambiri. Apa titha kunena kuti tabwera ndipo anyamata akulimbikira pa chilichonse." Anatero Chirwa.
KB tsopano yatsala ndi point imodzi kuti iyipeze Silver Strikers pomwe ili ndi mapointsi 35 pa masewero 23 omwe yasewera ndipo ili pa nambala yachisanu mu ligiyi.
"TIMAFUNA KUIMENYA WANDERERS KOMA OYIMBIRA SAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati oyimbira wayiteteza timu ya Mighty Mukuru Wanderers kuti isagonje ndi timu yake pomwe wati ziganizo zimakomera eni bwalowa.
Chirwa wayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yalepherana 1-1 ndi timu ya Wanderers ndipo wati chigoli cha Wanderers sichinalowe komanso ziganizo zina sizinali zokomera onse.
"Tasewera masewero, tinabwera kuti tiyimenye Wanderers koma oyimbira samafuna. Ziganizo zake zinali zokondera ngakhale mmene timayamba masewero komabe tinapeza chigoli ndipo mchigawo chachiwiri wapereka chigoli choti sichinalowe." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks ikuimabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 29 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino. Iyo yatenga mapointsi anayi pamwamba pa Wanderers mu ligi ya chaka chino.
#TAWONGA2023
"LIGI YATENTHA KOMA TILIMBIKIRA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati ligi ya TNM Supa ligi yatentha kwambiri pomwe zotsatira zikumakhala zozondoka koma ayesetsa kuti apeze zipambano zochuluka mu ligiyi.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Moyale Barracks 1-0 ku Rumphi ndipo wayamikira anyamata ake kamba ka chipambanochi.
"Anali masewero otentha kwambiri koma tiyamikira anyamata kuti apeza chipambanochi, mmene tinawauzira kuti tipeze chigoli mu mphindi 15 zoyambilira anapangadi." Anatero Chirwa.
Mphunzitsiyu watinso timu yake ikuyenera kupambana mmasewero awo akubwera kutsogoloku kuti adzamalize pabwino kamba koti ligiyi yatentha kwambiri. KB yafika pa nambala yachisanu ndi mapointsi 28 pa masewero 20.
Timu ya Kamuzu Barracks yalengeza kuti yasaina osewera wakale wa FCB Nyasa Bullets komaso Civo United, Nelson Kangunje.
Kangunje wasainira mgwilizano wa zaka ziwiri.
KB cut Bulletsβ lead - The Nation Online Β Second-placed Kamuzu Barracks on Sunday cut leaders Nyasa Big Bulletsβ lead to nine points at the top of the TNM Super League. The Peopleβs Team, who are... mwnation.com
Defender Herbert Wayekha has joined Kamuzu Barracks on a 3-year deal.
The former Silver Strikers defender is scheduled to resume training this week with the rest of Kamuzu Barracks squad.