"KUGONJA KWA LERO NDI KOPWETEKA KWAMBIRI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati timu yake yagonja mopweteka kwambiri pomwe wati point inali yabwino kwa iwo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 2-1 ndi Silver Strikers pa bwalo la Bingu lachinayi ndipo wati chigoli cha Chimwemwe Idana ndi chowawa kwambiri kumbali yawo.
"Ndi zoonadi tagonja masewerowa koma tagonja mopweteka kwambiri chifukwa kunali kutangotsala ma seconds moti kufanana mphamvu kunali kwabwino kwa ife komabe tingovomereza kuti zayenda motero koma zatipweteka kwambiri." Anatero Kalinda.
Iye anati timu yake iyesetsa kuti idzapambana mmasewero awo ndi Mighty Wakawaka Tigers kuti ilimbitse mwayi wawo othera pa nambala yaku mapeto. KB ili pa nambala yachinayi ndi mapointsi 45 pa masewero 29 omwe yasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores