"MU ZAKA ZIKUBWERAZI TIDZAKHALANSO PAMWAMBA" - KAWANGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Blessings Kawanga, wati timu yake sikuti yachita bwino kwambiri poti yatsika pa ndandanda poyerekeza ndi chaka Chatha koma wati kutsogoloku adzatheranso kumtundako.
Kawanga amayankhula atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers ndipo wati ndi zokhumudwitsa kuti mulingo womwe anapatsidwa ndi akuluakulu sanakwanitse komabe kutsogoloku ziyenda.
"Ndi zokhumudwitsa kuti chaka chinonso tilibe choti tiloze pa tebulo komabe zaka zikudzazi tiyesetsa kutero kuti mwina tibwererenso ngati zaka zammbuyomu kungoti mpira ndi wovuta poti umapanga zinthu zosiyana ndi zomwe tinakonza." Anatero Kawanga.
Timuyi tsopano yathera pa nambala yachisanu ndi mapointsi okwana 46 pa masewero omwe yasewera mu ligi ya chaka chimodzi. Aphunzitsi a timuyi anauzidwa kuti atengeko ka chikho kamodzi chaka chino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores