Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"OSEWERA ENA AKUMENYA NGATI AKUKAKAMIZIDWA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wandaula ndi mmene osewera ake achitira pa masewero awo ndi Moyale Barracks pomwe akuoneka ngati kuti akusewera ngati sakufuna chinachake kutimuyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Mzuzu pomwe timu yake inaphonya mipata yochuluka kwambiri mchigawo choyamba ndipo mchigawo chachiwiri Moyale inagoletsa ziwiri.
Iye wati: "Anali masewero abwino oti tikanatha kugoletsa zigoli mwina zinayi koma taphonya mipata yochuluka kwambiri nde mchigawo chachiwiri anzathu anakonza ndi kutigoletsa zigoli koma tinene pano kuti osewera ena akusewera ngati sakufuna." Anatero Kamanga.
Iye wati tsopano mpata womaliza mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi yavuta nde mmasewero otsiliza adzapereka Kwa osewera achichepere omwe akufuna kusewera mpira.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi pomwe yatolera mapointsi okwana 37 pa masewero 29 omwe yasewera.
"NAYENSO NKHAKANANGA WATENGAPO GAWO" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wadandaula kuti anthu amaloza chala timu ikagonja koma mmene anyamata ake aphonyera sizikufunika mphunzitsi komanso kuti Geoffrey Nkhakananga anapereka penate yabodza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Nankhaka masana a loweruka ndipo wati wavomereza kwakukulu kuti timu yake sinasewere bwino ndipo agonja.
"Kugonja kopweteka kwambiri ndipo inuyo atolankhani ndinu mumafalitsa mutha kuona mmene anyamata amaphonyera tiziti zikufunanso mphunzitsi? Masewero alero tangowapatsa a MAFCO, asewera bwino komabe ifeyo zativuta tivomere." Anatero Kamanga.
Iye wati aonetsetsa kuti masewero awo achite bwino omwe atsala nawo kuti mwina angathe kuthera pabwino mu ligiyi.
Kamuzu Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi okwana 37 pa masewero pa masewero 28 omwe yasewera mu ligi.
Win
"BULLETS INASEWERA BWINO KOMA MPIRA SUKUYENDA BWINO" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake yagonja chifukwa inakanika kuyigwira timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti isagoletse koyambilira komabe kayendetsedwe ka mpira sikali bwino mdziko muno.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Bingu ndipo wati anakonza kuti ayitchinge Bullets kuti isagoletse mu mphindi zoyambilira zenizeni koma zinavuta ndipo zinawabalalitsa.
Iye wati sakufuna kunamizira kugonjaku koma kusewera pafupifupi kukutopetsa osewera a timu yakeyi.
"Panopa zikuvuta chifukwa mpira tikusewera pafupifupi ndipo masiku 7 kusewera masewero atatu ndi zosagwira olo ku England sindikukhulupilira kuti zimachitika Izizi nde sikuti ndikunena kuti tagonja kamba ka izi koma zikufunika kuunikirapo." Anatero Kamanga.
Zateremu, timuyi tsopano yatuluka mu chikhochi ndipo FCB Nyasa Big Bullets yafika mu ndime yotsiriza ya chikhochi pomwe ikumane ndi Silver Strikers.
"TILEMBA MBIRI YATSOPANO YOMWE ANTHU ATADABWE" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati anyamata ake akonzeka kwambiri kuti apange mbiri yomwe sinachitikepo pomwe akufuna afike mu ndime yotsiriza ya Airtel Top koyamba lamulungu.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ya matimu anayi a mpikisanowu ndipo wati timu yake yakonzeka bwino mmasewerowa.
"Takonzekera bwino kwambiri kuti mwina tichite bwino pa masewero amenewa tikudziwa kuti akhala masewero ovuta poti tikusewera ndi timu yabwino koma ndime ngati iyiyi ndi yomwe timayesetsa kuti tichite bwino nde anyamata akonzeka." Anatero Kamanga.
Iye wati katswiri wawo womwetsa zigoli kutimuyi, Zeliat Nkhoma sapezeka mmasewerowa kamba kovulala koma onse alibwino kutimuyi.
Timu yomwe ipambane pa masewerowa idzakumana ndi timu ya Silver Strikers mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu yomwe yagonjetsa Mighty Mukuru Wanderers loweruka.
KAMUZU BARRACKS MATCH INTO CASTEL R16
Elite League side, Kamuzu Barracks, has become the fourth team to book a place in the round of 16 of the Castel Challenge Cup 2024 edition after beating Ntchisi Tigers 4-0 at the Nankhaka Stadium on Wednesday afternoon.
Gregory Nachipo put the Soldiers ahead on 13th minute before Redson Nkhoma doubling the scores from a free kick four minutes later as the hosts led 2-0 at half time. Substitute Sheriff Maulana won a penalty which Nkhoma converted for his second of the day on 64th minute before Maulana himself finding the back of the net with a powerful shot on 85th minute.
After the game, head coach for the Soldiers, Charles Kamanga thanked his boys for the win but said his team could have scored more than four in the match.
"It was a tough game but we have managed to win, I think we were underrating our friends because we could have easily scored more than four goals but I thank the boys for the win." Said Kamanga.
The result means Kamuzu Barr
"NDIKUKHULUPILIRA KUTI TIDZACHITA BWINO NDI BULLETS" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati akudziwa kuti masewero awo otsatira mu chikho cha Airtel Top 8 ndi FCB Nyasa Big Bullets adzakhala ovuta koma akonzekera bwino kuti adzachite bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa United 4-3 pa mapenate pomwe mmasewero onse awiri anathera 2-2 pa bwalo la Civo ndipo wati anali masewero ovuta pomwe kukonzekera kwawo kuti mchigawo choyamba adzagoletse zigoli zambiri sikunatheke.
Iye wati akudziwa kuti Bullets ndi timu yabwino koma timu iliyonse imafunitsitsa itafika mu ndime yotsiriza.
"Tikudziwa kuti adzakhala masewero ovuta kwambiri koma ndime ya matimu anayi imakhala yofunikira kwambiri ku timu iliyonse poti imafuna kufika mu ndime yotsiriza nde anyamata akudziwa mmene angachitire tikukhulupilira kuti tichita bwino." Anatero Kamanga.
Mu ndime ina ya matimu anayi ya Airtel Top 8, matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers adzak
Kb
"LERO TASEWERA NDIPO CHIGOLI TAZICHINYA TOKHA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wayamikira osewera ake kamba kosewera mwapamwamba ndi timu ya Silver Strikers ndipo wati Silver sinasewereko mpira wooneka pagolo pawo kupatula kuti azigoletsera okha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Silver lamulungu ndipo wati akonza mavuto awo ndipo ayesetsa kuti athere ndime zomwe adzapezeko ndalama mu ligiyi.
"Anyamata asewera bwino kwambiri ndipo ndiwayamikire kuti achita bwino ndipo Silver sinasewere pagolo pathu kupatula kuti tazigoletsera tokha koma ndi mpira momwe umakhalira tiwayamikire anzathuwa achita bwino apambana." Anatero Kamanga.
Iye anati timu yake ikadali ndi mwayi woti ithere pa nambala yabwino ndipo wati sangafike ku nambala yachisanu mu ligi poti iyo ndi timu yaikulu kwambiri.
KB tsopano yatsika kufika pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 31 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino.
KB YAFIKA PA NAMBALA YACHITATU
Nkhonya yobwenzera yawawa pomwe timu ya Kamuzu Barracks yakwanitsa kugonjetsa timu ya Chitipa United 2-0 pa masewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Nankhaka kuti ibwenzere chipongwe chomwe yakhala ikulandira.
Timuyi inagonja 4-1 mchigawo choyamba ndipo inabandulidwanso 2-0 mu chikho cha Airtel Top 8 lamulungu lathali koma zigoli za Samuel Chiponda ndi Gregory Nachipo zathandizira kutengera timuyi pa nambala yachitatu mu ligi.
Mphunzitsi wamkulu, Charles Kamanga, wati ndi wokondwa kamba Ka chipambanochi poti chikumakhala chosowa mu ligi.
"Anali masewero abwino kwambiri anyamata analimbikira kuti tipeze chipambano chifukwa Chitipa United ndi timu yabwino kwambiri koma tinayesetsa kuti tichite bwino chifukwa takhala tisakuchita bwino." Anatero Kamanga.
Iye anati chipambano chawo chakhala chofunikira chifukwa akwanitsa kusuntha mu ligi.
Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 31 pa masewero 20 omwe yasewera mu ligi.
KB ROPES IN TEMWA
The Yellow Submarine have taken on board coach Temwa Msukwa as First Assistant Coach (FAC)effective September 16.
There is minor shakeup in KB technical panel. Denis Kambewa who was FAC is now Second Assistant Coach (SAC) replacing Blessings Kawanga who is on other duties . Charles Kamanga remains HC
Temwa is well versed with KBFC philosophy having worked as interim HC and AC respectively. His main task is to bring the team back to glory .
“We as KB ,dismayed with the current performances of the Yellow Submarine, resoluted to take Temwa on board to help rejuvenate the team having considered several factors , commented KB General Secretary Albert Midian.
Temwa has already started working full throttle and will be in the dug out on Thursday afternoon against resilient Chitipa at Civo.
"WANDERERS DESERVED TO WIN" - KAMANGA
Kamuzu Barracks head coach, Charles Kamanga, has congratulated Mighty Mukuru Wanderers for recording a win over them in a game he believes the Nomads deserved a win.
He said this after suffering a 1-0 defeat at the Civo Stadium and said his team did not play in the game hence the defeat.
"It was a tough game we did not play well and let's congratulate Wanderers, they deserved to win. We struggled into the game and my boys failed to play according to our plan." Said Kamanga.
He further said his team still has a chance to fight for a better position in the league.
The soldiers are still on position 5 in the League with 28 points from 18 games they have played this season.
"TIMAKHULUPILIRA MBIRI NDIPO TIYIBWEREZA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake ili ndi mbiri yabwino kuti simagonja nthawi yochuluka Kwa Mighty Mukuru Wanderers ndipo akukhulupilira kuti mbiri izibwereza.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo pa bwalo la Civo ndipo wati timu yake ikudziwa kuti akhala masewero ovuta kwambiri koma ayesetsa kuti apambane.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri ndipo tikudziwa kuti akhala masewero ovuta poti Wanderers ibwera mwamkokomo koma tiyesetsa kuti tidzachite bwino. Ifeyo timakhulupilira mbiri nde tikukhulupilira kuti mbiri imeneyi tiyisunga kuti Wanderers siyitigonjetsa." Anatero Kamanga.
Iye wati kusapezeka Kwa osewera ngati Olson Kanjira sikukupereka mantha kwa iwo chifukwa ali ndi ena omwe alowe mmalo mwake.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 28 pa masewero 17 omwe yasewera mu ligi.
KB GETS FIRST WIN SINCE MAY 30
Kamuzu Barracks has ended its 8 game winless run with their first win since 30 May 2024 as they thumped relegation threatened Baka City 4-0 at the Aubrey Dimba Stadium on Sunday afternoon.
A brace from Sam Gunda and a goal each from top scorer, Zeliat Nkhoma and Gregory Nachipo were enough for the soldiers to record their 6th victory of the season.
Head coach for the team, Charles Nkhoma, said he was happy after his team ending their winless run that has stayed for almost three months.
"First let me thank the boys for playing according to what we told them, a win has done good for us as we last won on 30 May so we needed it much and I'm happy that we have finally gotten it." Said Nkhoma.
The Soldiers has jumped up to fifth position as they now have 28 points from 18 games they have played this season.
10 DRAWS, 8 GAMES WINLESS STREAK FOR KB
Kamuzu Barracks continues to struggle with form in the TNM Super League after recording their 10th draw of the season as they played a goalless draw against Karonga United at the Rumphi Stadium on Wednesday afternoon.
The Soldiers were looking for their first win in 7 games, having last won on 30th of May 2024 2-1 against the same team they faced today but failed to find a goal that could have eased their woes in the League.
After the match, Charles Kamanga, head coach for Kamuzu Barracks said his boys played well in the match but officiation denied them points in the game.
He said: "It was a tough game as I said before this match Karonga is also a good side but let me thanks my players, they really played well today despite not scoring but I am not happy with the officiation today." Said Kamanga.
The team missed the top goal scorer, Zeliati Nkhoma, who was not even on the bench and Kamanga said he didn't Impress during training.
"TAKHALITSA OSAWINA NDE TIYESETSA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake yakhalitsa osapeza chipambano ndipo akuyenera kuchilimika kuti achite bwino tsopano.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Karonga United pa bwalo la Rumphi lachitatu masana ndipo wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta koma akhala masewero asanu ndi awiri osapambana nde achilimika.
"Akhala masewero ovuta poti Karonga ndi timu yabwino ya ana achisodzera komanso ikusewera mpira wabwino koma ifeyo takhalitsa osawina, tasewera masewero 7 opanda kuwina nde tiyesetsa kuti tichite bwino ngakhale sizikhala zophweka." Anatero Kamanga.
Ndipo iye wati timuyi tsopano ili bwino pomwe yapeza ma goloboyi awiri, wotseka kumbuyo mmodzi ndi wosewera mmbali kuti athandizire kulimbitsa timuyi.
KB ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi okwana 24 pa masewero 16 omwe yasewera mu ligi.
"TIKHONZA KUSIMBA LOKOMA NDI CRECK" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati akuyembekezera kuti timu yake ichita bwino pomwe wakhutira ndi mmene anyamata ake achitira pa zokonzekera zawo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe asewere ndi Creck Sporting Club pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati timu yake yakhala osapambana pa masewero anayi nde ikuyenera kutero.
"Takonzekera bwino kwambiri komanso anyamata amaoneka kuti anali bwino ku zokonzekera zathu nde tikuyembekeza kusimba lokoma pa Dimba pomwe tikukasewera ndi Creck," anatero Kamanga.
Timuyi ili ndi mwayi wofanana mapointsi ndi Mighty Mukuru Wanderers mu ligi ngati angapambane chifukwa akhala ndi mapointsi 25.
Timuyi padakali panopa ili ndi mapointsi okwana 22 pa masewero 13 omwe yasewera pomwe yapambana kasanu, kufanana mphamvu kasanu ndi kawiri ndikugonja kamodzi.
"NDADANDAULA NDI OYIMBIRA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati oyimbira ayambe ntchito yotukula mpira mdziko muno pomwe wati wawathandiza atimu ya Premier Bet Dedza Dynamos kamba koti anali pakhomo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 2-2 pa bwalo la Dedza ndipo wati ndi okhumudwa kwambiri ndi zomwe oyimbira anachita powapatsa chigoli atimu ya Dedza.
"Ndi zokhumudwitsa kwambiri tikakhala kutukula mpira aziyambira oyimbira osati azikondera timu chifukwa choti ali pa khomo, chigoli chachiwiri inali offside koma oyimbira wawapatsa, opambana azipambana chifukwa analimbikira osati kuti wina wawapatsa ayi." Anatero Kamanga.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe yatolera mapointsi 22 mu ligiyi pa masewero 13 omwe yasewera.
"TIMAYENERA KUTI TIPAMBANE LERO" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake imayenera kuti apambane masewero awo poti anapanikiza mchigawo choyamba ndi chachiwiri chomwe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati timu yake inaphonya mipata yawo moti sikunalembedwe kuti apambane masewerowa.
"Takanika kupambana tokha, mpata unalipo pomwe tinapanikiza mchigawo choyamba komanso chachiwiri koma mwina mwayi sunali wathu kuti tipeze chipambano mmasewerowa." Anatero Kamanga.
Iye anatinso goloboyi wawo, Hastings Banda, wawathandiza kwambiri poti Bullets ikanatha kupeza zigoli zambiri komanso akufunikira kuti akonze kutsogolo kwawo.
Timu ya KB ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe tsopano ali ndi mapointsi 20 pa masewero khumi ndi amodzi (11) omwe yasewera.
"TIKHONZA KUWAGONJETSA PATAPITA NTHAWI" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake yakonzeka bwino kukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets loweruka ndipo litha kukhala tsiku loyamba kugonjetsa Maule patapita nthawi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Civo ndipo wati mavuto omwe ali ku Bullets si mwayi wawo kuti apambana mophweka koma akachilimika kuti akachite bwino.
"Ndi masewero ovuta kutengera kuti matimu tonse tikuchoka kofanana mphamvu nde aliyense akafuna chipambano koma ifeyo takonzeka kuti tikachite bwino. Nkhani zaku Bullets ndi zawo ndipo sikuti ziphweketsa masewerowa komabe ifeyo timangomaka kuti tikachite bwino." Anatero Kamanga.
Timu ya Kamuzu Barracks ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 10 omwe yasewera ndipo ikutsogola ndi mapointsi anayi pamwamba pa Bullets.