"ANALI MANGAWA KUTI TIKUNTHE CHITIPA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati timu yale inali ndi mangawa aakulu pa timu ya Chitipa United kuti apambane mmasewero awo kutsatira kuti iwo anagonja atapita ku Karonga mchigawo choyamba.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yapambana 2-0 pa bwalo la Kasungu ndipo wati apa tsopano akhonza kulengezano kuti KB yabwerano.
"Lero tapambana 2-0 Tithokoze Mulungu, kupambana kwa lero anali mangawa chifukwa anatimenya mchigawo choyamba pakwawo nde tinakonza kuti mchigawo choyamba tichinye zambiri. Apa titha kunena kuti tabwera ndipo anyamata akulimbikira pa chilichonse." Anatero Chirwa.
KB tsopano yatsala ndi point imodzi kuti iyipeze Silver Strikers pomwe ili ndi mapointsi 35 pa masewero 23 omwe yasewera ndipo ili pa nambala yachisanu mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores