"ZIKANAKHALANSO ZIGOLI ZITATU" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati timu yake imayenera kupambana poti yaphonya mipata yabwino koma wakondwera ndi mmene zotsatira zayendera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi Mighty Mukuru Wanderers ku Blantyre ndipo wati ndi okhutira ndi zotsatirazi.
"Ndine wokondwa kwambiri poti zayendera chonchi, moyenda kupeza point imodzi ndekuti zilibwino koma mwina tikanatha kupeza zigoli zitatu koma takanika kugwiritsa ntchito mipata yathu koma tikakonza zonse tikabwerera kunyumba." Anatero Kamanga.
Timuyi tsopano ili ndi point imodzi atasewera masewero amodzi ndipo yakhala pa nambala yachisanu ndi chinayi mu ligiyi.
Photo: Wanderers media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores