"TIMAFUNA KUIMENYA WANDERERS KOMA OYIMBIRA SAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati oyimbira wayiteteza timu ya Mighty Mukuru Wanderers kuti isagonje ndi timu yake pomwe wati ziganizo zimakomera eni bwalowa.
Chirwa wayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yalepherana 1-1 ndi timu ya Wanderers ndipo wati chigoli cha Wanderers sichinalowe komanso ziganizo zina sizinali zokomera onse.
"Tasewera masewero, tinabwera kuti tiyimenye Wanderers koma oyimbira samafuna. Ziganizo zake zinali zokondera ngakhale mmene timayamba masewero komabe tinapeza chigoli ndipo mchigawo chachiwiri wapereka chigoli choti sichinalowe." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks ikuimabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 29 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino. Iyo yatenga mapointsi anayi pamwamba pa Wanderers mu ligi ya chaka chino.
#TAWONGA2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores