"TILI NDI MKWIYO WOSALELETSEKA" - ALUFANDIKA
Mkulu woyang'anira aphunzitsi atimu ya Mighty Tigers, Robin Alufandika, wati timu yawo ili ndi mkwiyo waukulu pomwe ikuyamba masewero awo amu NBS Bank National Division League ndipo saleletseka akayamba kumenya matimu.
Abambo amayankhula patsogolo pa masewero awo oyamba mu ligiyi ndi Chilobwe United ndipo ati akuyembekeza kuyamba mwapamwamba.
"Za kukonzekera kwathu mphwanga zisiye, ifeyo tili ndi mkwiyo, mkwiyo wosaleletseka ndiye tiye uonere chifukwa mbambande ndi mbambande," anatero Abambo.
Iwo anatinso timu yawo inachivomereza kutuluka mu ligi yaikulu koyamba pa zaka 39 ndipo akuyembekeza kuti abwererenso posachedwa.
"Osewera otikondawo tikadali nawo Koma omwe sanatikonde anatithawa kukasaka malo kwinako komabe mbambande ndi mbambande tapeza osewera ena omwe atithandizenso kubwerera pomwe tinali paja," anapitiliza Alufandika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores