HAIYA WAFOTOKOZA NKHANI YA DERBY YA 2023
Mtsogoleri wa Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wafotokoza momveka bwino kusiyana kwa zomwe zinachitika mu 2023 zokhudza masewero a Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets ndi zomwe zachitika pano.
Haiya anayankha olemba nkhani atafunsa kuti naye ali ku Super League of Malawi anadelera FAM popitiliza masewero omwe FAM inaletsa ndipo anati ilo ndi bodza.
Haiya anati mu chakachi bungwe lomwe limavomereza mabwalo linavomera bwalo la Kamuzu ndipo masewero amachitika koma komiti yaikulu ya FAM, yomwenso iye analimo inangokhala ndi mantha kuti bwaloli lisamatenge anthu ambiri.
"A Pulezidenti nthawi imeneyo adanena kuti poti masewero akuluakulu amatenga anthu ambiri, bwalo lija litha kupanga ngozi. Awo anali mantha chabe koma a FIB anali atavomereza bwalo lija," anatero Haiya.
Iye wati zikusiyana ndi ulendo uno umene bwaloli lakanidwa malingana Kuti gawo lovomereza mabwalo laku FAM limagwira ntchito moima palokha ndipo iwo samakh
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores