Bullets iperekenso K1 million pogenda bus yawo
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu ya m'dziko muno la Super League of Malawi lapereka chilango ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti ipereke ndalama yokwana K10 million kamba koti ochemelera awo anagenda bus ya timuyi pa masewero omwe analepherana 3-3 ndi Karonga United.
Timuyi yalandiranso chilango chosasewera masewero asanu pa bwalo la Kamuzu komanso kupereka K5 million chomwe adzachigwire ngati abwereze kuchitanso mchitidwe wonga umenewu mu ligiyi.
Posachedwapanso SULOM inalipilitsa Bullets ndalama zokwana K4.75 million kamba koti wochemelera wawo analowa mu bwalo la zamasewero kukatenga thaulo la goloboyi wa Blue Eagles nthawi imeneyo, Joshua Waka.
Chithunzi: Blessings Chitekwere
0984871619
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores