CIVIL YAFIKA PA MWAMBA PA LIGI
Timu ya Civil Service United yafika pamwamba ligi ya FDH Premiership kutsatira kugonjetsa timu ya Ekhaya FC 1-0 pa bwalo la Civo mu mzinda wa Lilongwe loweruka masana.
Timuyi inapeza chigoli kudzera mwa wotseka kumbuyo John Dambuleni yemwe tsopano ali ndi zigoli ziwiri mu ligi kuti apate mapointsi onse atatu pakhomo.
Mphunzitsi watimuyi, Abbas Makawa, wati angakhale timu yake yapambana sinasewere bwibo mu masewerowa.
"Leroli sitinadzuke mwa mpira chifukwa zambiri zinatikanika, chokha chabwino tapanga ndi kupambana koma sitinasewere bwino," iye anatero.
Komabe Makawa wati akudziwa kuti masewero ena agonjako koma akufunitsitsa kumatolera mapointsi ochuluka mu masewero ambiri omwe azisewera.
Timuyi tsopano ili ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pomwe akwanitsa kupambana kawiri ndi kufananitsa mphamvu kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores