BAKA CITY YATENGA CHIKHO CHACHITATU MU 2023
Timu yomwe yangolowa kumene mu TNM supa ligi ya Baka City tsopano yakwanitsa kutenga zikho zitatu mu chaka cha 2023 pomwe yakhala akatswiri a chikho cha Nyasa Capital Finance chakumpoto atagonjetsa Iponga FC 1-0 mu ndime yotsiriza lamulungu.
Eddie Mwangama anagoletsa chigoli chokhacho pa mphindi zinayi za masewero omwe kuti timuyi ikhale akatswiri.
Ichi ndi chikho chachitatu chaka chino atatenga Mayors Trophy Ku Tanzania my mwezi wa July komwe anagonjetsa matimu amu dzikoli ndipo atenganso ukatswiri wa ligi yakumpoto yomwe yawatengera mu Supa ligi.
The Clever Boys ikuyang'ananso zotenganso chachinayi pomwe akumane ndi Wanderers Reserve mu ndime ya matimu anayi mu King Kabvina Trophy ku Dowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores