MWAUNGULU WACHIRA NDIPO ASEWERA NDI EKWENDENI
Katswiri mbambande wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Patrick Mwaungulu, akuyembekezeka kuonedwanso pa bwalo la zamasewero lachitatu atasowa kwa sabata imodzi pomwe tsopano wachira pa kuvulala kwake.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Heston Munthali, watsimikiza za kubwereranso kwa mnyamatayu patsogolo pa masewero awo ndi Ekwendeni Hammers mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Castel ndipo wati anyamata onse akonzeka.
"Tikukumana ndi timu ya Ekwendeni yomwe titakumana mu ligi chapompano tinavutika nayo ndekuti akhala masewero ovuta kwambiri koma anyamata tawauza kufunikira kwa masewerowa kuti tikawamaliziretu kuti tipite chitsogolo nde takonzeka." Anatero Munthali.
Iye watinso anthu asaikiretu kuti Bullets yadutsa kale mmasewerowa poti masewero amu chikho amakhala ovuta kwambiri. Opambana pa masewerowa akuyembekezeka kukumana ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu ndime ya matimu anayi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores