KHUMALO WAPITA KU ZAMBIA
Katswiri wotseka kumbuyo kutimu ya Scorchers komanso Silver Strikers Ladies, Ireen Khumalo, akuyembekezeka kukhala wosewera wa Green Buffaloes kwa chaka chimodzi pomwe wasaina mgwirizano pangongole kutimuyi.
Timu ya Silver Strikers yatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la mchezo lachiwiri kuti katswiriyu akatumikira tsopano mu FAZ Women's Super league ku Zambia.
Iye anapita ku Silver Strikers chaka chomwe chino kuchokera ku Ascent Academy ndipo wakhala ofunikira kwambiri mu ligi ya chaka chino kutimuyi pomwe ali pa nambala yachitatu pambuyo pa MDF Lioness ndi Ascent Academy.
Iye analinso mu gulu la osewera omwe anatenga ukatswiri ndi timu ya Scorchers wa COSAFA Women's Championship mmiyezi yapitayo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores