NYAMILANDU WAFUNIRA ZABWINO HAIYA
Mtsogoleri yemwe wangochoka kumene Ku Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, wamufunira zabwino yemwe walowa mmalo mwake, Fleetwood Haiya, pamene akuyamba kugwira ntchito yake.
Iye walankhula izi kudzera mu kalata yake atagonja pa zisankhozi ndipo iye wati ndi wokondwa poti akuchoka mpira ulibwino kusiyana ndi mmene anaupezera.
Iye wathokoza amalawi polora kuti atsogolere mpira wamiyendo mdziko muno pomwe anakwanitsa kupanga zinthu zingapo zobweretsa chimwemwe kwa amalawiwa.
Haiya wakhala woyamba kuchotsa Nyamilandu yemwe anayamba kulamulira kuchokera mu chaka cha 2004.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores