PHODO, MFUNE NDI CHIYENDA SAPEZEKA NDI RED LIONS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati osewera ake atatu, Maxwell Gasten Phodo, Antony Mfune komanso goloboyi Rabson Chiyenda sapezeka pa masewero omwe akumane ndi Red Lions kamba kovulala.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe achitike pa bwalo la Balaka lachitatu ndipo wati anyamata ake akonzekera kuti akachite bwino mmasewerowa.
"Anyamata akonzekera bwino kuti tikapambane, tikukumana nawo oti ali pa chiopsezo choti atha kutuluka komanso amatipatsa mavuto komabe tikuyenera kupita ndi mtima wonse kuti tikapambane." Anatero Munthali.
Timu ya Bullets ikungofunako mapointsi asanu ndi imodzi (6) kuti apambane ligi ya chaka chino pa masewero asanu omwe atsala nawo kuti amalize ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores