"UKAYENDA MASEWERO AMAKHALA OVUTA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Heston Munthali, wati timu yake yasewera bwino komabe akakhala kuti akasewera koyenda amadziwa kuti masewero amakhala ovuta kwambiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Nankhaka ndipo wati masewerowa anali ogundana kwambiri mpake sanasewere bwino.
"Tithokoze osewera athu poti tapeza point imeneyi, anali masewero ovuta kwambiri mchigawo choyamba sitimakhazikitsa mpira pansi koma mchigawo chachiwiri tinapeza mipata yomwe taphonya. Anali a masewero a physical kwambiri ndi zoti osewera athu amafunika kutetezedwa komabe ma Yellow card ambiri apita kwa ife iwo ayi." Anatero Munthali.
Timuyi yatsala ndi masewero atatu kuti imalize ligi ya chaka chino ndipo ili ndi mapointsi 56 pa masewero 27 omwe yasewera. Timuyi ikutsogola ndi mapointsi awiri pamwamba pa Mighty Mukuru Wanderers.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores