"SITIKUDANDAULA KUTI TAGONJA SIZIKUOPSA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake sikudandaula kuti agonja ndi Ekwendeni Hammers mu ligi ya TNM pomwe wati sizikuopsa kuti atha kutuluka.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-2 pa bwalo la Rumphi ndipo wati amadziwa kuti akhala ndi masewero ovuta nde ayang'anabe mmasewero awiri omwe atsala nawo.
"Tagonja inde komabe tiwayamikire anyamata kuti asewera bwino, timadziwa kuti akhala masewero ovuta potengera ndi manambala a matimu onsewa koma takwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri koyenda, anyamata agwira ntchito." Anatero Chidati.
Timuyi ikadali pa nambala 10 mu ligi ya TNM ndi mapointsi okwana 33 mu ligiyi ndipo ikufunikira kupambana mmasewero awo omwe atsala nawo kuti alimbitse mwayi wotsalamu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores