Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yaimitsa wapampando wa Komiti ya masapota atimuyi dziko lonse, Stone Mwamadi, kamba kokhudzidwa ndi nkhani yomwe ili mmanja mwa apolisi.
Mwamadi anamangidwa pamodzi ndi mkulu wa masapota a Wanderers pa Stand, Yonah Malunga, kamba kowaganizira kuti anakakamiza mkulu wa wayilesi ya MBC kuti apepese kwa mtsogoleri wa dziko lino, Prof. Arthur Peter Mutharika.
Timuyi yati yachita izi polola kuti nkhaniyi ifufuzidwe bwinobwino komanso posunga mbiri yabwino ya timuyi yomwe imadana ndi za ntopola zili zonse.
A Mwamadi pamodzi ndi a Nayo awatulutsa kaye pa belo kudikira kuti milandu yawo iyendetsedwe ku bwalo la milandu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores