"TIKUYEMBEKEZERA MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Mponda, wati akuyembekezera masewero ovuta kwambiri pokumana ndi timu ya Silver Strikers komabe alimbikira kwambiri ndi kuti apeze chipambano pa masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akudziwa kuti kusewera kwa timu ya Silver mu CAF kuwapatse ukadaulo ndi mangolomera pa masewerowa koma akathana nazo.
"Phuma lilipo osati kuti ndinali komweko ayi koma iwowa ndi timu yaikulu yomwenso ikusunga chikhochi zomwe zikuonetsa kuti sangangobwera nkutipatsa mapointsi panonso apeza ukadaulo wambiri ndi mu CAF nde phuma lilipo koma tingoona kuti tithana nalo bwanji," anatero Mponda.
Iye wati osewera atimuyi onse alipo kupatula Crispin Mapemba pomwe wati zimakhala zabwino kuti osewera ochuluka akhale ali bwinobwino.
Bullets ili pamwamba pa ligi ndi ma points okwana 43 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligiyi ndipo Silver ili ndi 36.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores