"NKHANIYI TITHANA NAYO BWINOBWINO - CHIGOGA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yati otsatira timuyi sakuyenera kudera nkhawa pa chilango chimene timuyi yalandira kuchokera kubungwe la FIFA ponena kuti nkhaniyi athana nayo bwino bwino.
Kudzera mu chikalata chimene bungwe la FIFA lalembera Bullets pankhani yokhudza kontirakiti pakati pa timuyi ndi Ronald Chitiyo, FIFA lapereka chilango choti Bullets isasaine osewera aliyense pa misika itatu kutsogoloku ngati simulipira osewerayu ndalama zokwana K27.2 million.
Albert Chigoga, mkulu woyendetsa ntchito za timuyi, watsimikiza kuti nkhaniyi siyodetsa nkhawa kwambiri chifukwa ikupereka danga loti akhoza kuthana nayo mopanda chovuta chilichonse.
"Sinkhani yoti anthu adwale nayo mutu kapena ayambe kumwa Panado chifukwa chigamulochi chikufotokoza bwino lomwe kuti pokhapokha ngati sitilipira ndalama zimene atiuza ndipamene adzatiletse kusaina osewera akuno komanso akunja." Chigoga Anafotokoza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores