"Osewera asamasankhe masewero oti alimbikire" - Chatama
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati osewera a timu yake anabwera odelera kumaona ngati agonjetsa kale timu ya Mzuzu City Hammers pomwe kulimbikira panalibe kuchititsa kuti agonje mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 pakhomo kuti ayambe mchigawo chachiwiri mwa udyo ndipo wati kusalimbikira kwa osewera kwachititsa kuti agonje.
"Sitimayenera kugonja Koma anyamata anabwera ndi mtima woti apambana kale kuti chipambano achipeza mophweka poti Hammers ili kummusi Koma tachinyitsa zigoli zophweka kwambiri, mtima wolimbikirawo panalibe, osewera asamasankhe masewero oti azilimbikira." Anatero Chatama.
Iye Koma wati timuyi ikufunikira wosewera osewera kutsogolo kuti azisunga mpira zomwe zizithandizira kuti asamataye mipata yochuluka ngati momwe achitira lero.
Timuyi ikadali pa nambala yachinayi mu ligi pomwe ili ndi ma points okwana 26 pa masewero 16 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores