"LERO LUANAR INALI BWINO KWAMBIRI" - MSAKAKUONA
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles De Klerk Msakakuona wati zinali zovuta kwambiri kuti timu yake ichite bwino kamba koti timu ya LUANAR Mitundu inali bwino paliponse kuyamba mpaka kumaliza pa masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-2 kuti akanike kuonjezera mapoints awo pamwamba pa ligi ya FDH Premiership pa bwalo la Dedza loweruka masana.
Iye wati timu yake inayesera kusintha akugonja 1-0 koma zinathera kugoletsetsa zigoli ziwiri ndipo zinali mochedwa kuti abwenze mu masewerowa.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa tinali achiwiri pa mpira ndipo LUANAR inali bwino paliponse kuyamba mpaka kumaliza ndipo amayenera kupambana masewerowa," anatero Msakakuona.
Iye wati timu yake tsopano yachinyitsa zigoli zisanu pa masewero awiri zomwe zikufunika kukonzedwa kamba koti samachinyitsa mu masewero awo oyamba.
Timuyi ikadali pamwamba pa ligi ndi mapoints 16 pa masewero asanu ndi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores