"CIVIL TIMAYIPATSA ULEMU KOMA SITIMAYIOPA" - MSUKWA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers Mapopa Msukwa wati masewero awo ndi Civil Service United akhala ovuta kamba koti anzawowo akhala pakhomo komanso kuti osewera amadziwana koma akonzeka kuti akapambane.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Civo mu FDH Premiership ndipo wati akonzeka.
Iye wati timu yake sikhala ndi Felix Demakude, Eric Atsigah komanso Andrew Joseph kamba kovulala koma ali ndi osewera ena omwe agwire ntchito pa malo pomwe palibe enawo.
"Ndi masewero ovuta chifukwa anzathuwo abwera mwa mphamvu kamba koti tinawachinya masewero onse chaka chatha komabe taika njira zoti tikachite bwino mmasewerowa," anatero Msukwa.
Iye watinso masewerowa ndi ofunikira kuti achite bwino chifukwa mpikisano mu ligi wavuta zomwe sizikufunika kumataya mapoints.
Silver ikupita mu masewerowa ili pa nambala yachiwiri pomwe ili ndi mapoints 13 atapambana kanayi, kufananitsa mphamvu kamodzi nd
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores