Katswiri wosewera mmbali watimu ya Flames, Chifundo Mphasi, wasankhidwa kukhala wosewera yemwe wazikokera kwambiri kutimu ya Power Dynamos mu Chaka cha 2025-26.
Mphasi wasankhidwa pa mwambo womwe timuyi inakonza kuti ipereke mphoto kwa osewera ake kutsatira kupambana chikho cha MTN Supa Ligi.
Katswiriyu anali wofunikira pomwe amathandiza timuyi popita kutsogolo ndi zigoli zinayi komanso kuthandizira zisanu ndi chimodzi kuti apate mphotoyi.
Mu zaka ziwiri zomwe wakhala ndi timuyi, iye wapambananso ligi kawiri zomwe ili mbiri yabwino ya iyeyo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores