Bungwe la MAGLA lalowa mu mgwirizano ndi bungwe la Super League of Malawi kuti lizipereka mphoto kwa osewera omwe agoletsa chigoli chapamwamba pa mwezi komanso wotchinga pagolo wochotsa mpira maukadaulo pamwezinso.
SULOM lalengeza za nkhaniyi lolemba mammawa pa tsamba lawo la Facebook ndipo yati mgwirizanowu ndi wa ndalama zokwana K40 million.
Bungweli lati izi zithandizira kwambiri kukweza luso la osewera ndi otchinga pagolo mu ligimu poti ziziwalimbikitsa kwambiri.
Osewera yemwe wamwetsa chigoli chabwino kwambiri pa mwezi azilandira K1 million chimodzimodzinso goloboyi yemwe azichotsa mpira mwaluso kwambiri pa mwezi azilandiranso K1 million.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores